Chichewa

‘Kudali kosungitsa ndalama’

Listen to this article

Ena ukamalowa m’banki amangoganiza kuti chaphindu chochoka mmenemo ndi kusunga kapena kutapa ndalama komatu ena akusimba lokoma chifukwa tikukamba pano ali pa banja lokoma.

Sadock Ng’ambi wa ku Chitipa yemwe amagwira ntchito yoonkhetsa chuma kubungwe la Unesco akuti amakaika ndalama za bungweli kubanki ndipo mwamwayi adakumana ndi Tumenye Mwenitete wa ku Karonga yemwenso amakasungitsa ndalama.

Awiriwa akuti adakhala pa mzere umodzi m’bankimo ndipo amacheza ngati adadziwana kalekale apo kudali kukumana kwawo koyamba ‘mwinatu chilankhulo chidagwilapo ntchito’.

Mpaka imfa kudzawalekanitsa:  Sadock ndi Tumenye
Mpaka imfa kudzawalekanitsa: Sadock ndi Tumenye

“Adandisangalatsa momwe adamasukira nane ndipo mumtima ndidangomva kuti tseketseke. Mmene amamwtulira, timanyazi pang’ono ndi sangala ndidaona ndekha kuti koma mkazi ndi uyu,” adatero Sadock.

Iye adati panthawiyo m’chaka cha 2010 sadathe mawu adangopempha nambala ya lamya ya mmanja yomwe adalandira naye nkupereka yake ndipo kuyambira apo udali ubale ochezerana pa lamya.

Ataona kuti bobobo amuzulitsira boonaona adalimba mtima nkupita kukaonekera kwawo kwa Tumenye ndipo monga mwa mwambo wa kwawo adapereka malowolo nthawi yomweyo kuti ena asowe khomo lolowera.

“Nditapereka malobolo, padapita chaka china ndipo mchaka cha 2012 ndi pomwe tidamanga woyera ku Kawale CCAP ndipo madyerero ake adali kusukulu ya sekondale ya Chipasula,” adtero Sadock.

Iye adati akaona mkazi wakeyo amakhala ngati waona makolo ndi abale ake chifukwa cha chikondi ndi chisamaliro chomwe amalandira.

Naye Tumenye sadafune kuotcha chofunda koma kuyamikira ndi kuthokoza kuti

adapeza mwamuna wakukhosi kwake.

“Ambiri alipo okwatira ndi kukwatiwa koma ineyo pandekha ndimadzitenga

wodala. Mwinanso ena amadzitenga odala mmaanja awo ndiye kuti nawo adapeza wawo ngati mmene ndidapezera wanga,” adatero Tumenye.

Tikunena pano awiriwa ndi bambo ndi mai aulemu wawo, opemphera komanso okondana ngati mkazi ndi mwamuna.

Related Articles

Back to top button
Translate »