Chichewa

‘Kudali ku FDH Bank’

Listen to this article

Zina ukamva umakhala kaye jenkha ndi kulingalira kuti kodi makamaka zikuchitikazi ndi zoona kapena ntchedzera chabe. Koma poti suzumile adanka naye ndi zomwe zidamuchitikira Elton Nkhulande pomwe ankasaka woti amange naye banja.

Padali pa 4 September 2018 pomwe iye adakumana ndi Edith Nthala mu FDH Bank ku Linga, Nkhotakota boma, Elton akuti atangomuthira diso mtima wake udavutika kwambiri ndi maonekedwe ake.

Iye adamuphinyira diso la kumanzere. Komatu mbetayo idasonyeza kunyansidwa, ndipo sadafunenso zoti ndimulankhulitse, motere zidatengera kulimba mtima kwanga potengera maonekedwe ake komanso pozindikira kuti mpira n’kumaka.

Elton ndi Edith kuthyola dansi paukwati wawo

“Nditangotuluka m’banki ndidamudikira panja kuti amalize zochita zake, motere padatenga mphindi 30 kuti atuluke. Komatu nditayamba kuponya mawu ankaoneka kuti sankasangalala ndi zomwe ndinkamuuza. Panthawiyo n’kuti ndili pa galimoto ya kuntchito, ndipo makiyi adali m’manja poganizira kuti mwina ulendo wofuna namwaliyo ukhale ophweka koma chiyembekezo changa ndi malingaliro ake zidasemphana ndithu,” adatero iye.

Elton, yemwe ankagwira ntchito kuchipatala cha St Annes, adamufunsa kumene ankakhala, ndipo adati kwa Malasa komwenso sikudali kutali ndi komwe naye ankakhala.

Komatu padatenga miyezi itatu mnyamatayo akutsata njoleyo ndipo padatenga miyezi itatu kuti apeze nambala yake, apa ndiye kucheza kudafika pena mpaka Edith adathyola khosi.

“Zidandipatsa chidwi poona ndi mmene ankalimbikirira kunditsata ndi kumandifunsa kuti andikwatire, ndipo ndidalimba mtima kuti zitero motsimikiza mtima wanga nditaona nthawi ndi nyengo yomwe yadutsa,” adatero Edith.

Awiriwa adayamba moyo watsopano pa 14 December chaka chatha, pomwe adamanga oyera ndi kuvekana mphete.

Edith yemwe ndimphumzitsi pasukulu ya pulaimale ya Chisoti m’bomalo ndipo adabadwa m’chaka cha 1991. Iye ndi woyamba kubadwa m’banja la ana 5.

“Moyo wathu wa m’banja ukuyenda bwino kwambiri, poyamba zinali zovuta ndi chilendo poti zokonda zinali zosiyana, koma pano ayi ndithu zonse zili bwino ndithu ndipo kusunga khosi ndi zoonadi mkanda woyera ndiye ndavala,” adatero iye.

Elton ndi wachisanu kubadwa ndipo amachokera kudera la mfumu Chiboko, T/A Mphonde m’boma la Nkhotakota ndipo akugwira ntchito ku AG Care ngati woyendetsa galimoto. Awiriwa ndi Akhristu a mpingo wa Anglican.

Related Articles

Back to top button