Chichewa

Kudali Ku Karonga

Listen to this article

 

Pamene ena amati chikondi sichiona chikhalidwe kapena mtundu wa khungu la munthu, banja la Manaseh Chisiza, mkulu wa bungwe la azisudzo ndi mkazi wake Andrea Beyerlein likuchitira umboni mawuwa.

Manaseh, mkulu wa National Theatre Association of Malawi, adakumana ndi njole yake ku Karonga komwe Andrea adabwera ndi makolo ake kuyendera ntchito zachifundo zomwe iwo adali kugwira mogwirizana ndi bungwe lina la ku Mzuzu.

Manaseh ndi Andrea tsiku la ukwati wawo
Manaseh ndi Andrea tsiku la ukwati wawo

“Atabwera nthawiyo adapezeka kuti adafikanso ku Lusubilo Orphan Care Project komwe ndidamuona koyamba,” adatero Manaseh, yemwenso ndi mkulu wa gulu la zoimb la Lusubilo Band.

Awiriwa adapatsana nambala za telefoni ndipo ankachezerana kufikira pomwe adakumananso ku Germany chaka chathachi.

Kukumana kwawo ali ku Germany kudali chiyambi cha chikondi chomwe chidakula ndipo chikukulirakulirabe mpaka adamanga woyera mwezi watha ku Germany komweko.

Manaseh adati Andrea yemwe ndi woimba komanso wochita mafilimu amalemekeza chikhalidwe chake Chimalawi ndipo banja lawo limaganizira zikhalidwe zonse za Chizungu komanso chikhalidwe cha Chimalawi.

“Andrea amakonda kukonza m’nyumba pomwe ine ndimakonda kuphika osati chifukwa cha chikhalidwe cha kwawo koma chifukwa ndimakonda kuphika basi kuyambira kalekale ndipo ndimaphika bwino kwambiri,” adatero Manaseh.

Manaseh ndi wochokera m’mudzi mwa Khwawa T/A Mwasambo m’boma la Karonga ndipo adabadwa m’banja la ana 8 momwe ndi wachisanu ndi chimodzi kubadwa. Andrea adabadwa yekha m’banja la kwawo.

Related Articles

Back to top button