Chichewa

‘Kudali ku mapemphero a Scom’

Listen to this article

Patha zaka zisanu tsopano Dyson Milanzie yemwe ndi mkonzi wa mapologalamu kuwailesi ya kanema ku MBC-TV ali pabanja ndi njole yake Jane.

Awiriwatu adamangitsa woyera pa 30 July 2011 ku Word Alive Garden mumzinda wa Blantyre.

Adakumana ku BSS: Dyson ndi Jane
Adakumana ku BSS: Dyson ndi Jane

Dyson amakhulupirira kuti Mulungu ndiye adagwira ntchito yonse kuti iwo akumane ndi kumanga woyera.

Iwo adadziwana m’chaka cha 2003 pomwe Jane amaphunzira kusukulu ya sekondale ya Blantyre (BSS), Dyson ali kusukulu ya pulaiveti ya Kamacha koma onse n’kuti ali Fomu 2.

M’chakachi sukulu ya Dyson idakonza mapemphero a Students Christian Organization Malawi (Scom) omwe amakachitikira ku sukulu ya BSS. Kupatula mapemphero, Dyson adagwiritsira ntchito nzeru zachibadwidwe pamene adaponya maso pa Jane.

Macheza okhudza mapemphero adayambira pomwepo, koma mosakhalitsa zinthu zidasintha, Dyson adaganiza zolankhula nkhani ina kwa njoleyi ndipo mu 2004 Dyson adafunsira njoleyi koma tsoka ilo adakana.

Izi akuti zidabalalitsa Dyson chifukwa maso ake amalasalasa pa njoleyi kotero kudali kovuta kuti ayang’ane kwina.

Mnyamatayu sadalekere pomwepo, adayeserabe kuponya Chichewa chake ngakhale chimakanidwa koma mu 2005 pamene njoleyi imaphunzira pa koleji ya Polytechnic, akuti mpomwe idalola Chichewa cha Dyson.

Jane akuti loto lake lidali lodzagwa m’chikondi ndi mwamuna wokhulupirira Mulungu. Iye akuti ataonanso kuti kupemphera kwa Dyson sikudali kwachinyengo, adaganiza zomulola.

Kukhulupirira Mulungu akuti ndicho chakhala chinsinsi chawo kuti lero angakwanitse zaka zisanu popamba kuponyerana mapoto kapena kuitana ankhoswe kuti adzaweluze milandu.

Awiriwa ati achinyamata azizisunga ngati akufuna kudzagwa m’manja a munthu woopa Mulungu.

Dyson Milanzie ndi wa m’mudzi mwa CheMgundo kwa T/A Kumtaja m’boma la Blantyre ndipo ndi wa 9 m’banja la ana 11.

Jane Milanzie wa m’mudzi mwa Bwese 2 kwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu ndi wachiwiri m’banja la ana asanu. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »