Chichewa

Kudali ku sitolo ya ‘Peoples’

Listen to this article

 

 

Khalidwe la Gift Simkonda lokonda kukagula katundu kusitolo ya Peoples kwa Magalasi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre m’chaka cha 2010 lidathera kwa mnyamatayu kuzulamo nthiti yake, Eunice Chingoni.

Panthawiyo nkuti Eunice akugwira ntchito ya pa till m’sitolomo pamene Gift adali akugwira ntchito ku sitolo za Dapp ngati wophunzitsa anthu za mmene angamachitile malonda ku Ndirandeko.

Malinga ndi Eunice, nthawi zonse akaona Gift akulowa musitoloyo, mtima wake umakankha mwazi mwaliwiro kulakalaka mnyamatayu atadzakhala wakumkeka wake koma poti ndi mkazi sakadalankhula kotero amayesetsa kumuchitira mkomya musitolo momwemo pomudindira komanso kumulongezera mnyamatayu katundu bwino mujumbo akagula katundu.

Banja la Simkonda tsiku la ukwati
Banja la Simkonda tsiku la ukwati

“Zinkandiwawa Gift akapita podinditsira mitengo pamunthu wina chifukwa ndinkadziwa kuti sindimva mawu ake komanso sandiona,” adatero Eunice.

Iye adati, chimene chinkamuzula moyo kwambiri mwa Gift ndi lilime lake la Chitumbuka, maonekedwe ake ofatsa komanso kuumbidwa bwino kwa mnyamatayu.

Naye Gift adati mtima wake udayamba kuthawathawa m’malo ngati netiweki ya lamya za m’manja atasiyanitsa umunthu umene nthandayi idali nayo pa makasitomala kufikira pamene naye adayamba kudyerera maso padonalo.

Gift adati kupatula kudzichepetsa komanso nsangala zimene zidakuta wakumkeka wakeyu, mnyamatayotu akutinso ankakopeka ndi dzino logamphuka limene lili mkamwa mwadonalo limene limaonekera akamamwetulira.

“Nditayizindikira nyenyeziyi sindidachedwe koma kupatsana nayo nambala ya foni ndipo patadutsa masiku tidagwirizana kuti tikumane kuti ndikatule nkhawa zanga pa iye,” adatero Gift.

Koma Gift akuti adakhumudwa ataponya khoka lake la chikondi mudziwe la chikondi la njoleyi pamene duwali lidatemetsa nkhwangwa pamwala kuti silikufuna kugwa mchikondi ndi iye.

“Ndidakana dala ngakhale pansi pamtima ndinkadziwa kuti ndikumufuna. Ndinkafuna kuonetsetsa kuya kwa chikondi chake paine ndipo pakutha pa miyezi iwiri ndi pamene ndidampatsa makiyi a mtima wanga,” adatero Eunice.

Nkhani ya awiriwa itafika m’makwawo kuti akufuna akwatirane idautsa mapiri pachigwa chifukwa akwawo kwa Eunice, mngoni, sankafuna akwatirane ndi mtumbuka ndipo akwawo kwa Gift sankafuna kuti mwana wao akwatirane ndi mngoni.

Awiriwa adati zidali zopweteka kwambiri ngati dzino lobooka kuzimvetsetsa kuti asakwatirane chifukwa cha kusiyana chilankhulo ndi mtundu.

“Pafupifupi chaka chinadutsa anthu akwathu atatisiyanitsa koma sitidakhale chete tidayetsetsa kuwaunikira kuti chikondi adalenga ndi Mulungu ndipo Mulunguyo ali ndi mphamvu yolumikizanitsa anthu amitundu yosiyanasiyana ndikukhala thupi limodzi. Tidali okondwa anthu ambali zonse ziwiri atatimvetsetsa ndikutilola kuti titengane,” adatero Gift.

Awiriwa adamangitsa woyera pa August 4 2013 ndipo ali ndi mwana mmodzi, Wongani, amene akwanitse chaka chimodzi chaka chino. Banjali likukhala ku Zomba kumene Eunice akugwira ntchito ku sitolo ya Peoples ya Matawale pamene Gift akugwira ku Dapp ya mumzinda wa Zomba.

Gift amachokera m’mudzi wa Muyereka kwa T/A Wasambo ku Karonga pamene Eunice ndi wa m’mudzi wa Chingoni kwa mfumu yaikulu Mpando ku Ntcheu ndipo akulangiza anthu kuti maziko a mabanja awo akhale chikondi osati kumene amachokera kapena chilankhulo chawo chifukwa izi zimachititsa munthu kukwatirana ndi munthu amene sumamukonda.n

Related Articles

Back to top button