Chichewa

‘Kudali kukwaya ku Mtima Woyera’

Listen to this article

 

Udali ulendo wokhetsa thukuta lowopsa kuti zonse zilongosoke pakati pa Gray Lizimba ndi Iness Chimombo koma zonse zidafika pampondachimera Loweruka lapitali pomwe awiriwa adapatsana malonjezano omaliza.

Inde, pamtendere ndi pamavuto, moyo wabwino kapena matenda sadzasiyana. Awa ndiwo adali malonjezo pakati pa Gray ndi Iness omwe amachokera ku Bembeke m’boma la Dedza ndipo onse amachita bizinesi mumzinda wa Lilongwe komanso amayimbira limodzi kwaya ku Mtima Woyera Parish ya mpingo wa Katolika mumzinda wa Lilongwe.

Gray akuti ulendo udayamba m’chaka cha 2009 awiriwa atakumana kutchalitchi ndipo Gray sadafune kuchedwa koma kufunsira pomwepo koma akuti sizidayende.

“Adandiyankha kuti ndisadzayerekeze kumulankhulanso za nkhaniyo, koma sindikadakwanitsa kutero. Mtima wanga udali pa iye ndipo ndidapitiriza kutchetcherera mpaka mu April, 2012 mpomwe adandilola,” adatero Gray.

Gray ndi Iness kupsopsonana patsikulo
Gray ndi Iness kupsopsonana patsikulo

Iye adati atangomva mawu oti ‘ndavomera’ adamva ngati wanyamula dziko lonse m’manja mwake, mtima ukudumphadumpha uku m’masaya muli chimwemwe chokhachokha.

Iye akuti adakhala pachibwenzi mpaka m’chaka cha 2014 mwezi wa November pomwe awiriwa adapanga malonjezano oyamba pachinkhonswe ndipo adagwirizana kukhala zaka zina ziwiri asadapange ukwati kuti akonzekere mokwanira.

“Kuchoka apo tinkakonzekera ukwati wathu ndipo tonse tidaikapo mtima mpakana zonse zidatheka pa 4 June, 2016. Tidakadalitsira ku Mtima Woyera ndipo madyerero adali kubwalo la St Peter’s Anglican ku Lilongwe,” adatero Gray.

Iye akuti Iness ndi chimwemwe komanso ufulu wake chifukwa amamulimbikitsa m’zinthu zambiri ndi kumuthandiza m’maganizo pomwe mutu waima.

Iness sadafune kunena zambiri koma kungotsimikiza kuti iye ali ndi chimwemswe kuti mtunda womwe adauyamba zaka 7 zapitazo wafika pampondachimera.

Iye adati kuchoka tsiku lomwe awiriwa adakumana, adziwana kwambiri ndipo saona chomwe chingabwere pakati pawo kudzasokoneza chikondi chawo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »