Chichewa

Kudali kumapemphero a achinyamata’

Listen to this article

Munthu aliyense ngakhale atakhala wachisodzera imakwana nthawi yomwe amayenera kusiya kusereula ndi kuchita zinthu zogwira mtima.
Sam Sambo, ngakhale adali wachisodzera, adakhala adalimba mtima pamene adakumana ndi Emelia Chaula pofuna kumuuza za kumtima kwake.

Watengeratu basi: Sam ndi Emelia patsiku la ukwati wawo
Watengeratu basi: Sam ndi Emelia patsiku la ukwati wawo

Emelia ndi mphunzitsi wa kupulaimale pomwe Sam akugwira ntchito ndi bungwe la God Cares Orphan komanso amachita zisudzo ndipo ndi wapampando wa bungwe la Theatre Association Northern Chapter.
Sam atamuona Emelia sadaugwire mtima koma tsiku lomwelo adamuuza za kugunda kwa mtima wake podziwa kuti bobobo samuthandiza ndipo akachedwetsa ena angamulande njoleyo.
Sam adati iye adamuthira diso koyamba Emelia kumapemphero a achinyamata ndipo naye msungwana sadachedwe kugonekera khosi Sam atamuuza mawu achikondi.
Mnyamatayu adalonjeza kuti iye wake ndi Emelia ndipo akazi ena adalibe nawonso ntchito ndipo kuchokera pomwepo Sam sadayang’anenso akazi ena kufikira tsiku la ukwati wawo.
Awiriwa adamanga woyera kumpingo wa St Andrew’s CCAP ku Mzuzu ndipo madyerero adachitikira pa Victory Temple ku Mzuzu komweko pa 11 July chaka chino.
Sam adaululira Msangulutso kuti iye adagwa m’chikondi ndi Emelia kaamba ka mtima wake wolimbikira ndi wodzipereka pantchito ya Mulungu.
Emelia amachokera m’mudzi mwa Kawazamawe, Themba la Mathemba (Paramount Chief) Chikulamayembe m’boma la Rumphi ndipo ndi woyamba kubadwa m’banja la ana asanu. Sam ndi wa m’mudzi mwa Yobe Sambo Inkosi Mtwalo m’boma la Mzimba ndipo ndi wachiwiri kubadwa m’banja la ana asanunso.
Banja latsopanoli lati silikufuna banja losalimba ngati mabanja ambiri amasiku ano ndipo iwo anenetsa kuti nthawi zonse aonetsetsa kuti akuika Mulungu patsogolo. Iwo ati nthawi zonse akakhala ndi vuto amayang’ana kwa Mulungu osati kupita kwa anthu omwe akhoza kukulitsa kavuto kakang’ono.

Related Articles

Back to top button
Translate »