Chichewa

Kudzula: Mpeni wofunikira kwa butchala

Popha mbuzi kapena ng’ombe amagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana monga nkhwangwa, zikwanje ndi mipeni. Umodzi mwa mipeniyi umatchedwa ‘kudzula’ ndipo eni ake akuti mpeniwu amagwiritsa ntchito posenda nyamayo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Innocent Chimsewu yemwe amapha n’kugulitsa nyama ya mbuzi kuti adziwe chinsinsi chosagwiritsa mpeniwu pantchito zina koma kuphera ndi kusendera nyama basi. Iwo adacheza motere:

Tandiuze dzina lako ndi ntchito yomwe umapanga, mnyamata.

Dzina langa ndine Innocent Chimsewu ndipo ndimapha mbuzi ndi kumagulitsa nyama yake mumsika wa ku Area 22A ku Lilongwe.

Kodi pali zinsinsi zilizonse zokhudzana ndi bizinesi ya nyama makamaka ya mbuzi kapena ng’ombe?

Chimsewu kusenda mbuzi ndi  mpeni wa kudzula
Chimsewu kusenda mbuzi ndi mpeni wa kudzula

Ndikudziwa zomwe mukutanthauza ngakhale mukukhala ngati mukukuluwika pang’ono ndipo yankho lake ndi ili: bizinesi ya nyama ya mbuzi kapena ng’ombe n’chimodzimodzi bizinesi ina iliyonse. Apa ndikutanthauza kuti momwe anthu amayendetsera bizinesi ina iliyonse, ndimoso zimachitikira m’bizinesi ya nyama.

Ndidamvako kuti mpeni wosendera nyama ya malonda sugwiritsidwa ntchito zina, zimenezi n’zoona?

N’zoona, mpeni umenewu tikamaliza kusendera mbuzi kapena ng’ombe timautsuka bwinobwino kuusunga pamalo abwino kuti usamalike. Kunena zoona si kuti pali kugwirizana kulikonse koma kuti anthu amangochita izi ngati njira imodzi yosamalira mpeniwu kuti usasowe.

Dzina la ‘kudzula’ lidabwera bwanji?

Ndi dzina basi monga momwe maina ena onse amayambira kapena kubwerera. Ena adangoganiza kuti mpeniwo ukhale kudzula mwina potengera ntchito yomwe umagwira yosendera nyama.

Umakhala mpeni wooneka bwanji?

Ndi mpeni monga momwe umakhalira mpeni wina uliwonse koma uwu umakhala wakuthwa kwambiri komanso kawirikawiri, umaning’a mmphepete imodzi ngati wosokera nsapato kaamba konolanola. Timanola pafupipafupi chifukwa mpeni wobuntha umanyotsola nyama posenda. Mnofu wambiri umatsalira kuchikopa.

Ndikubwezere mmbuyo pang’ono. Mpeni wa kudzula utasowa, mpeni wina uliwonse sungagwire nthito yosendera mbuzi kapena ng’ombe?

Ukhoza kusendera bwinobwino popanda choletsa. Komansotu posenda mbuzi kapena ng’ombe si kuti pamakhala mpeni umodzi wokha, ayi, kungoti si mipeni yonse yomwe ili kudzula, koma wokhawo womwe ndalongosola uja ndipo umenewu ndiwo suloledwa kugwiritsa ntchito ina iliyonse

Ntchito ina ya kudzula ndi chiyani?

Kudzula amagwira ntchito zambiri pakupha ndi kusenda mbuzi ndi ng’ombe. Ntchito yoyambirira ndi yothyolera fupa la pakholingo. Wocheka pakhosi akacheka, pamakhala fupa lomwe limatsalira lomwe limasunga moyo ndiye amatenga kudzula n’kuthyolera fupa limeneli. Ntchito ina, poti mpeniwu umakhala wakuthwa kwambiri, ndi kuchekera zam’mimba monga mtima, chifu, matumbo ndi ndulu. Makamaka pa ndulupo, ukagwiritsa ntchito mpeni wobuntha, mwangozi ukhoza kuthudzula ndulu ndiyetu kungotero, ndiwo yonse yaonongeka.

Nanga mubutchala mogulitsira nyamayo kudzula safunika?

Si kwenikweni, iye kwake nkophera ndi kusenda koma zikavutitsitsa akhoza kugwira ntchito yochekera mubutchala si kuti china chake chingachitike, ayi, koma kuti ambiri amaumira kutero kuopa kusowetsa.

Related Articles

Back to top button