Nkhani

Kugwiririra ana kudzatha?

Listen to this article

Pafupufupi tsiku lililonse tikumamva kapena kuwerenga malipoti akuti mwana wagwiririridwa penapake.

Omangidwa akumangidwa. Kugwira ndende ndiye kosakamba koma zikuoneka kuti zilango zomwe zinaikidwa kwa ogwirira anthu zikulephera kuthetsa mchitidwewu.

Kuphatikiza apo, pali zilango zina zoti anthuwa akapatsidwa iwe wakumva umagwa nazo mphwayi kapena kukhumudwa kumene.

Malamulo a dziko lino amati chilango chokulitsitsa kwa munthu wogwiririra mwana wochepera zaka 14 ndi kukakhala kundede moyo wake wonse pamene wopezeka wolakwa pongofuna kugwiririra mwana, amayenera kukakhala kundende zaka 14.

Ngakhale malamulowa ali chonchi, pali ena oti akagwiririra mwana amangopatsidwa ndede ya zaka zitatu kapena zisanu.

Ngakhale makhoti ali ndi mphamvu zosiyana pakaperekedwe ka chilango, pakuyenera kupezeka njira ina yoonetsetsa kuti ogwiririra ana apatsidwe ndende yowawa.

Zilango zing’onozing’onozi zapeputsa nkhanza yogwiririra ana ndipo zikulephera kuopseza ena ofuna kugwiririra ana.

Mwachitsanzo, wina akauzidwa ndi sing’anga kuti chizimba chopezera chuma ndi kugwiririra mwana, n’kwapafupi munthuyu kupirira ndende ya zaka zisanu chifukwa aziti ndikatuluka kundede ndidzasambira m’chuma choposa.

Koma kugwiririridwa ndi chipsinjo chosaiwalika kwa olakwiridwa ndipo ena amatha kusokonekera mutu kumene.

N’chifukwa chake maiko ena amaika dongosolo loti anthu ochitiridwa nkhanzayi athandizidwe ndi akatakwe a momwe munthu amaganizira kuti moyo wawo usasokonekere.

Izi ndi zina zomwe unduna ndi mabungwe oona za ana angamaganizireko kuchita pambali powerengetsa ana amene akuchitiridwa nkhanza zamtunduwu.

Koma koposetsa malingaliro alunjike popeza njira zoti munthu aziopera kutalitali kukhudza mwana mosayenera.

Njira yapafupi ndiyo kukhwimitsa chilango kwa ogwiririra ana powapatsa ndende ya moyo wonse kapenanso kuwadula ziwalo zimene akuononga nazo miyoyo ya ana osalakwa.

Related Articles

Back to top button
Translate »