Chichewa

Kuikira kumbuyo khalidwe loipa

Listen to this article

 

Zimanenedwanenedwa zinthu ngati izi kwa amayi okwatiwa:

“Osamasiyira Anaphiri kuti azingophikira abambo, kenaka akulandani banja…”

“Osaleka kudzisamalira chifukwa bamboyo maso alunjika pena…”

“Pakhomo kumasamalira chifukwa uve umathamangitsa bambo…”

Izi ndi zitsanzo chabe, koma pali zambiri zomwe mzimayi amachenjezedwa kuti asamalitse pofuna kusunga banja.

Tikaonetsetsa palibe vuto ndi kusamala pakhomo, kudzisamalira ndi zina zotero, koma nzolakwika kuika zinthuzi ngati zida zothandizira kuti bambo akhazikike pakhomo.

Chifukwa polankhula motere—ndipo izi zimalankhulidwa kwambiri m’malo achilangozo—timakhala ngati tikuvomereza kuti zina mwa izi ndi zifukwa zoyenerera popangitsa kuti bambo azinka nachita zibwenzi chifukwa mkazi wake walephera penapake kunyumba.

Kunena zoona abambo ena amakhala ndi zofooka  zina zikuluzikulu zomwe amayi amazipirira m’makomomu osaganizirakonso kuti mwina apeze mpumulo popeza chibwenzi.

N’chifukwa chiyani zimaoneka zabwinobwino kuti abambo azilephera kupirira nkhani ngati za chakudya n’kufika pomasirira Naphiri kuti mpaka apange naye chibwenzi chifukwa waphika bwino?

Abambo otere ngachimasomaso ndipo amakhala kuti Naphiriyo amamusirira kale. Ndiye malankhulidwe omamuuza mkazi kuti akulekerera amakhala akuikira kumbuyo makhalidwe onyansa.

Pali abambo ena autchisi, ena oti akavula nsapato fungo nyumba yonse. Sudzamupeza mayi akuti bola Joni okonza maluwa amadzisamalirako. Mmalo mwake mayi amayesetsa kuti akonze nsapato ndi sokosi za mwamuna wake kuti fungo lichepe.

Koma mzimayi akamveka thukuta, ndiye bambo ali ndi chifukwa chomveka bwino choti akasake chibwenzi? Osamuuza mkazi wako za vuto lake nkuthandizana naye kupeza njira zothetsera fungo la thukutalo bwa?

Mundimvetse, sindikuti amayi atayirire, koma tizindikire kuti amayi amakhala ndi zofooka. Tsono zofooka za amayi zisakhale zifukwa zokwanira zoti abambo azinka nasaka akazi ena.

Related Articles

One Comment

  1. Zikomo kwambiri mayi Rabeca kamba kokambapo pa nkhani iyi. Ndiyamikire maganizo anu abwino zedi ndithu. Koma ineyo monga bambo ndimangofuna ndipemphe kuti tonse abambo ndinso amayi tiyenera kuzama pophunzira chilengedwe cha mwamuna ndinso mkazi. Anthu amene amalangiza azimai motere ndiyesa adazindikira kuti mwamuna chikoka chachikulu chili 1. pa zomwe akuona koposa zomwe akuuzidwa. Mwina mpamene pamabwera mau oti akazi ndi maluwa adziko (meaning a man is more attracted by what he sees than what he hears). Chonco ndithu mayi Rabeca yesetsani kuamalitsa umo mukuonekera komanso kusamalira pakhomo. 2. Amayi nthawi zambiri chikoka chawo chimakhala pa zomwe akumva. Nchifukwa chake akazi ambiri amakopeka ndi mau owayamikra (sweet talk than zomwe akuona). Komanso mbali zonse (makamaka amuna) amava bwino koposa kupangilidwa chinthu ngakhale chingaoneke chochepa e.g kumuchapira bambo zovala kwaiye it means a lot than zovala zomwezo kukachapitsa ku laundry. Ndizovuta kumvetsa koma this is the psycho-social aspect of males and females. Ndiye ngakhale ndovomereza kuti amuna sitiyenera kutenga izi ngati zinthu zothandizira kuyamba mchitidwe wachisawawa ndafuna ndigwirizane nawo anthu amene amalangiza azimayi pankhani yozisamalira ndinso working for their homes. Zikomo

Back to top button
Translate »