Chichewa

Kulakwa, kulakwatu pa Wenela!

Listen to this article

 

Tsikulo lidali lokumbukira asungwana ndi amayi oyendayenda ndipo tidazunguliradi mumzinda wa Lilongwe. Tidali ndi Abiti Patuma kuti ationetse monse.

Kudalitu kuyenda, kuzungulira apo akuti pa Matchansi (kaya ndiye kuti chiyani), kukafika uko ku Culture Club, komanso uku kwa Biwi, mpaka komwe ku Chigwirizano ndiponso pa Bwandiro, inde paja pa Ma China komanso ku Likuni ndi Chigwirizano sikuti tidaphonyako. Mukanena za Bwalo la Njovu ndiye osanena, apo pa Akazembe komanso hotela yopanda zipinda zogona ija, ndiye osaiwala m’mwamba muja mumakhala anthu odikira kukwera Ta’qwa ngakhalenso a nsomba. Lilongwe!

Nanga ndikuuzeninso kuti tidafika ku Mzuzu? Pa Dziwazako zidalipo! Nanjinanji pa Sports Café! Eisssh, uku ku Mlambe Inn ndi Paris Club!

albino-art

Kudalitu kuyenda. Mpaka tidafika ku Chitipa. Kumenekotu Moya Pete amatsegulira mpita. Nanga inu mumayesa ndinatsala mu Lilongwe? Mwandiona chiyani?

Ndipo kumenekonso sitidakhaleko nthawi. Tidabwerera kwathu ku Wenela. Pajatu kwathu kudasintha, si kwa Kanduku! Kwathu nku Wenela.

Chongofika pa Wenela, tidapeza mkulu wina akunena kuti wangochoka ku Lilongwe kumene mkulu wachikwama amabwebweta izi ndi izo zachuma. Kodi mkulu ameneyu sanatopebe? Kodi iyeyo, chikwama ichi timaona atanyamula chaka ndi chaka sichimulemera? Nanga bwana wamtundu wanji wopanda chola boyi? Bwana wamtundu wanji kupanira bulifikesi, kapena mwati ndi sutukesi?

Nanga amakanenanji? Amanena chiyani uyu mdala? Zaka zitatu akuyankhula zosamveka koma timagoti komabe!

Ndinaiwala. Titafika ku Chitipa, tidamva kuti Moya Pete wati Kamacha wapita ku Tanzania kukaphunzira za momwe tingagwirire awa akupha abale anzathu achialubino!

Kulakwa.

Nanga akaphunzirako chiyani? Akatenga chiyani? Kodi mmesa kalelo tinkati ankangosowa?

Kulakwa.

Kudya posalima.

Kulakwa.

Nanga izi zoletsa asing’anga zadza ndi yani? Kodi nkhaniyi ndi ya ung’anga?

Adafika mnyamata wina pa Wenela ndi chikwama chake. Adandiitanira pambali.

“Akulu, ndikufuna kuchita nanu bizinesi. Tikudziwa muli ndi 15 mita. Tikangopeza mafupa a 10 mita, inutu muyiphula! Tikagulitsa 50 mita pena pake,” adatero.

“Zabwino. Koma ndimufunse kaye Abiti Patuma,” ndidamuuza.

Kulakwa.

Kulakwa.

“Kodi iwe sukudziwa kuti awawa ali ngati aja ankagulitsa mankhwala osambitsira mahatchi? Sukudziwa kuti iwowa ali ngati aja ankagulitsa diamond m’tauni ya Blantyre ndi Lilongwe? Sukudziwa kuti awa ndi anyamata a chintambalala? Apolisi akuwadziwa kale anyamatawa nanga mpaka kupita dziko lakuti likufuna kutilanda nyanja? Ndipo mwati chaka chino sindilandira feteleza?” adatero Abiti Patuma.

Palibe icho ndidatolapo koma ndidamugwira pakhosi mnyamata adabwera ndi mafupa uja! Ndidamugwetsera uko!

Kulakwa! Kulakwa!

Fupa la munthu silingabweretse chuma ngati uli waulesi!

Gwira bango! Upita ndi madzi!!! Mawa tikupeza, muja tidapezera uja wodula mawere! n

 

 

Related Articles

Back to top button