Nkhani

Kulambira Kalonga Gawa Undi

Listen to this article

Tamvapo zambiri za mwambo wa Kulamba. Mongokumbutsana, Kulamba ndi mwambo womwe mafumu Achichewa m’maiko a Malawi, Mozambique ndi Zambia amapezerapo danga lokapereka uthenga wa mmene zinthu zikuyendera m’madera awo kwa mfumu yawo yaikulu, Kalonga Gawa Undi. Lero tati tisanthule zina ndi zina zomwe zimaloledwa kuchita ndi kusachita pamaso pa mfumu ya Achewayi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu kumwambo wa Kulamba wa chaka chino motere:Gawa-Undi-by-Stanely-makuti-Mana

Ndikudziweni mfumu.

Ine ndine Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu pakati pa Achewa a ku Malawi ndipo ndimachokera m’boma la Kasungu.

 

Tandifotokozerani zokhudza ulemu wa Kalonga Gawa Undi kuyambira mmene mumaperekera moni.

Kalonga Gawa Undi ndi mfumu yaikulu kwambiri pakati pa Achewa kotero kuti ulemu wonse womalizira pakati pa Achewa umayenera kupita kwa Kalonga Gawa Undi. Pachifukwa ichi, palibe munthu aliyense yemwe amaloledwa kugwirana chanza ndi Kalonga Gawa Undi pokhapokha kalongayo atayamba yekha kupereka mkono koma sayenera kukhudzidwa mwanjira iliyonse.

 

Nanga popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi zimakhala bwanji?

Uwu ndi mwambo wina wapadera womwe umafunika kusamala kwambiri. Popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi munthu amayenera kuika mphatsoyo pansi kapena pagome lomwe lakhazikitsidwa mwini wake akuona. Akatero, imodzi mwa nduna zake za kalongayo amakatenga mphatsoyo n’kukaika pamalo oyenera, osati kumupatsira m’manja, ayi. Nthawi zonse kumakumbuka kuti kalonga ndi munthu wamkulu.

 

Nanga pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kutani?

Pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kukhala pansi chotambalala osati chokhwinyata, ayi. Ngakhale mipando itakhalapo yambiri motani munthu amayenera kukhala pansi pokhapokhapo ngati mwini wake kalongayo wakukakamiza kuti ukhale pampando. Ngati uli Mchewa weniweni, ngakhale Kalonga atakukakamiza chotani, umayenerabe kukana ndi kukhala pansi basi, koma n’kofunika kukumbukira kutambalala, osapinda miyendo pamaso pa Kalonga Gawa Undi.

Nanga ungatani kuti Kalonga Gawa Undi akupatse mpata wolankhula naye?

Funso limeneli limavuta nthawi zambiri chifukwa anthu amaona ngati Kalonga Gawa Undi amangolankhula chisawawa. Pomwe Kalonga waperekera mpata wolankhulana naye si pano ndipo ngati ukufuna kulankhula naye umayenera kuomba m’manja ndi kulankhula mokwenza mawu akuti: ‘Yooh,

Gawa!’ katatu ndipo ngati ali ndi mpata akhoza kukupatsa mwayi wolankhulana naye.

 

Nanga ngati mfumu yaikulu ya Achewa, ubale wake ndi wotani ndi gulewamkulu?

Choyamba, gulewamkulu alibe mphamvu iliyonse kwa Kalonga Gawa Unidi, chimodzimodzinso naye, ngati kalonga, alibe nthawi yopanga za gulewamkulu. Ntchito imeneyi amalekera mafumu ake kuti aziyendetsa. Kalonga akamayenda amayenera kuzunguliridwa ndi mbumba zake (amai oimba nyimbo).

 

N’chifukwa chiyani mbumba, osati nduna?

Pamwambo wa Achewa amayi ndiwo amakhala ndi mphamvu zosankha mfumu. Pachifukwachi, amayi amapatsidwa ulemu wapadera chifukwa popanda iwo kasankhidwe ka mfumu kamasokonekera. Kalonga Gawa Undi amadziwa zonsezi ndiye pofuna kulemekeza udindo womwe amayi ali nawo, n’chifukwa amafuna kuti mbumba ndizo zizimuperekeza.

Related Articles

Back to top button
Translate »