Chichewa

Kulimbana ndi alaliki

Listen to this article

Ndidakhala pa Wenela tsikulo kubwira mpweya, uku ndikuitanira basi.

“Ndirande iyi! Machinjiri iyo! Ntcheu-Balaka cha uko!!!” ndidali kutero.

Pajatu masiku ena ndikati ndilowe three engine, kuitanira basi zitatu nthawi imodzi zimatheka.

Ya Ntcheu-Balaka ija itadzaza, ndidapita ndikatenge zanga. Kaya ikafika ku Balaka ndilibe nazo ntchito. Ngakhale itapezeka kuti pofika pa Mdeka mwangotsala anthu atatu, zingandikhudze?

art

Nditafika uko ndidapeza munthu wa Mulungu akulalikira, keupempherera apaulendo kuti ayende bwino.

“Ndikunena pano ziwanda za pamsewu zakonzeka kukulikhani. Ziwanda za pa Linthipe zakonzeka kumwa magazi anu ngati simutetezedwa. Inde ziwanda zochoka pansi pa madzi zikusautsani ngati simulapa,” adali kutero mlaliki.

Abale anzanga, ulaliki wamtundu wanji uwu wokhala ngati amalankhula nazo ziwanda? Kodi mlaliki ameneyu atati wakatumikira kuchipatala, sanganene kuti: “Inu ochimwa inu! Lapani lero lino nditi lapana. Ngati simutero, zifuwa zanuzo zikutengerani kugahena. Kuchita kusaweruzika kwanuko, wa kumoto basi.”

Ndi mwayi omwe kuti utumiki wa kuchipatala udamusempha. Kodi sindinganene kuti akuopa kuti kuchipatalako sakatulukako ndi loboola ilo amapeza pano pa Wenela?

Nkhani ya alaliki ili mkamwamkamwa ndi ya mlaliki Makala Funeral. Mumudziwa bwino woimba uja ankakamba za mfumu Betisezala ndi zolembalemba pakhoma. Tikumva kuti zinavutatu uko ku Mangalande.

Mwachidule, zikumveka kuti mlaliki adacheza ndi mnzake wa Abiti Patuma wina pangongole ndiye lero nkhani yonse ili pa mbalambanda.

“Akungomulakwira mlaliki. Tikudziwa ankamwa, kusuta mpaka kugona m’chimbudzi kalelo koma anali asanalape. Lero taonani nkhani zikuphulikazi!” adatero Abiti Patuma titakhala malo aja timakonda pa Wenela madzulo a tsikulo.

Apa nkuti akundionetsa zithunzi ndi mavidiyo pafoni yake akuonetsa chikondi cha mlaliki ndi uyu msangwana wa kwa Msamati.

“Nkhanizi zikumavuta kuyankhira. Kukhala ngati chiwanda choipa chalowa pamudzi pano. Taonani mudabweretsa za uyu wojambula mizimu, wopalasa mlengalenga, naye uyu wa matama ndi galimoto zake! Tsono mukutinso bwanji za mlaliki wathu wa ku Chilomoni?” adafunsa Gervazzio.

Musandifunse kuti nkhaniyi imayenda bwanji chifukwa nanenso sindikudziwa. Chomwe ndikudziwiratu nchakuti awa ndi masiku otsiriza ndipo kuyalutsa anthu a Mulungu ana a njoka ena akuchitenga cha fasho.

Chonsecho akusiya Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe akupitiriza kuwaula tonse pano pa Wenela ndi mfundo zokhwima. Akusiya Adona Hilida akupitiriza kuthawa mudzi wawo omwe ati kukashaina ndi JT ndi ena otero, mudzi wawo ukufa ndi njala! Inde, akusiya Lazalo Chatsika ndi Male Chauvinist Pigs akuwuwa koma osaluma ngati galu wokulira kumpanda! Zoona, akusiya Cheka Chitenje ndi Kile Kabudula wa Chiwaya akudya za renti molapitsa!

Pano pa Wenela anthu ogona achulukitsa!!!

Gwira bango! Upita ndi madzi iwe!

 

Related Articles

Back to top button