Nkhani

Kulira, chimwemwe ndi banki m’khonde

Listen to this article

Ngakhale adali ndi chidwi choyamba bizinezi kuti atukuke, kusowa kwa mpamba kumapondereza khumbolo. Sanderson Yuba wa m’mudzi mwa Namalima kwa T/A Nazombe m’boma la Phalombe adakanika kutenga ngongole kubanki kaamba kosowa chikole komanso kuopa chiongola dzanja chokwera.

Lero mkuluyu ndi mmodzi mwa makhumutcha m’deralo kutsatira ngongole yomwe adatenga kubanki m’khonde ndi kuyamba bizinezi ya matabwa mpaka wamanga nyumba ya malata, kugula njinga ya moto ndi ziweto.

Mabanki m’khonde afalikira m’dziko muno

“Kupanda banki m’khonde loto langa loyamba bizineziyi si likanakwaniritsidwa. Bwenzi pano ndili mpopangolo wa m’mudzi. Bankiyi idandithandiza kupeza mpamba,” adatero Yuba.

Yuba ndi mmodzi mwa Amalawi omwe miyoyo yawo yasintha chifukwa cha mabankiwa. Koma si onse otenga nawo mbali akusimba lokoma, ena akumana ndi zikhomo kutsatira kusokoneza ngongole zawo za banki m’khonde ndipo ali muumphawi.

Mmodzi mwa iwo ndi Janet Mawata wa m’boma la Phalombe lomwelo  yemwe atakanika kubwenza ngongole ya K20 000 adalandidwa katundu.

Mayi wina, yemwe anati tisamutchule dzina, ku Zomba adalandidwa nyumba kaamba ka ngongole ya K250 000 ndipo padakalipano umoyo wake ukuvuta.

Pakutha pa chaka, m’mizinda ndi m’matauni anthu akumagawana ndalama zochuluka, ena mpaka K7 miliyoni, kuchoka kubanki m’khonde. Koma ndalamazi zimasungidwa m’nyumba mwa membala wosankhidwa kutero, osati kubanki.

Izi zidachititsa mkulu wakale wa banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve Bank of Malawi (RBM), Charles Chuka kunena kuti mabanki m’khonde sakufunika chifukwa akusokoneza kayendedwe ka chuma.

Mabungwe ena atsutsa izi.

Mkulu wa Community Savings and Investing Promotion (Comsip) bungwe lomwe limayang’anira mabanki m’khonde, Tenneson Gondwe, adati kutero ndi kusokoneza cholinga cha ndondomekoyi yomwe imapereka mpata wa ngongole kwa anthu osowa.

“Anthuwa amasonkha ndalama zomwe amabwerekana ndi kuyamba mabizinezi komanso kugawana pakutha pa chaka. Kulowerera kwa RBM kungasokoneza miyoyo ya anthu. Ngati akufuna angopanga banki ya kumudzi yomwe izikwaniritsa zosowa za anthu,” adatero Gondwe.

Kafukufuku wa bungwe la Finscope adapeza kuti anthu 50 pa 100 ali onse m’dziko muno ali ndi kuthekera kofika ku mabanki a pamwamba koma 21 pa 100 wo ndi amene ali ndi mabuku ku mabankiwo.

Zotsatirazi zikupereka mpata kumabanki m’khonde kukhala ndi anthu ochuluka poonjezera chiongola dzanja chochepa chomwe amapereka pa ngongole iliyonse. 

Related Articles

Back to top button