Nkhani

Kulumana pa ofunika kulandira chakudya

Listen to this article

Kusankha ovutikitsitsa kuti alandire thandizo la chakudya kuchokera ku boma kwavuta m’midzi ina pamene anthu ndi mafumu ayamba kulumana.

Izitu zadza pamene boma kudzera m’nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma) yayamba kugawa chakudya kwa anthu amene sadakolole chakudya chokwanira chifukwa cha ntchemberezandonda ndi ng’amba.

Kugawa chimanga kuli mkati m’maboma ena

Nthambi ya Dodma idapempha alangizi a zamalimidwe komanso ofesi ya DC m’boma lililonse kuti itolere maina a anthu amene athiphwa ndi njala.

Pa ntchitoyo, Dodma idatolera mabanja oposa 400 000 malinga ndi amene akuyendetsa ntchitoyi ku Dodma, Paul Kalilombe.

“Awatu ndi anthu oposa 2 miliyoni amene tikuyenera tiwapatse thandizo. Iyi ndi nambala yomwe tigwiritse ntchito dziko lonse,” adatero Kalilombe.

Koma nambalayi yakhumudwitsa mafumu ena amene akuti m’madera awo asiya anthu ambiri amene akhudzidwa ndi njala.

Gulupu Cheghama wa m’boma la Karonga kwa Paramount Kyungu adati m’dera lake anthu a mwa nyakwawa 5 ndi amene akhudzidwa ndi njala ndipo ayenera thandizo madzi asadafike m’khosi.

Cheghama adati anthu pafupifupi 300 ndi amene akuphupha ndi njala mwa mfumu Ngingekemo, Mwangwabila, Kazguli, Kazguli 2 ndi Mwaphoka.

“Chomwe tadabwa ife n’chakuti ngakhale tidapereka mainawo kuti boma liwathandize, iwo avomereza anthu 75 okha kuti ndiwo alandire chakudya,” adatero Cheghama.

Gulupu Mpochera ya kwa mfumu yaikulu Tsikulamowa m’boma la Ntcheu yati idapereka maina a anthu 250 amene adakhudzidwa ndi njala m’dera lake.

Poyamba akuti adadziwitsidwa kuti nambala ija ayidula ndipo anthu 115 ndi amene alandire thandize.

“Sabata yatha adaitananso mafumu onse, titapita akatiuza kuti nambala ija ayidulanso ndipo anthu 45 okha ndi amene alandire thandizo,” adatero Mpochera.

“Anthu 250 tonse takambirana kuti chimanga chikabwera, tonse tikhala pansi ndipo tigawana. Kaya aliyense adzatenga chimanga chodzadza mbale yokha bolani akaphike kaphala ndi kumwa,” adaonjeza.

Mfumuyo idati dera lake kapuchi ndi ng’amba ndi zimene zidasokoneza moti palibe amene adapeza ngakhale thumba limodzi la chimanga.

“Kunoko kuli moto, ineyo ndimakolola matumba oposa 10 koma chaka chino ndidapeza ndowa imodzi basi,” adatero iye.

Koma Kalilombe akuti nthambi yawo ikuyang’ana anthu okhawo amene alibe pogwira ngakhale ‘nkhuku yeniyeniyi’ alibe.

“Zoti chiwerengero chabwera chochepa bwanji ife zimenezo sitikudziwa chifukwa tidadalira ena kuti afufuze amene akufunika thandizo ndipo nambalayo tidapatsidwa.

“Komanso zoti chimangacho azigawana gulu ife sitikondwera chifukwa ndiye kuti akupha cholinga chathu kuti anthu asafe ndi njala. Anthu ena angovomereza basi kuti si onse amene angalandire thandizo,” adatero Kalilombe.

Iye adati pa banja la anthu pafupifupi asanu likulandira thumba limodzi la chimanga lolemera ndi makilogalamu 50.

Lipoti la Malawi Vulnerability Assessment Committee (Mvac) lomwe lidatuluka mwezi watha lidati anthu 3.3 miliyoni atuwa ndi njala chaka chino chifukwa choti anthu sadakolole chakudya chokwanira.

Kodi anthu enawo athawira kuti? Kalilombe akuti akamaliza gawo ayambalo, akhala pansi kuti aunguze za anthu 3.3 miliyoni amene Mvac yafunthula.

“Amene tikuwagaira pano sitidagwiritsire ntchito zomwe yatulutsa Mvac, koma tikamaliza gawoli ndiye kuti tikhala pansi kuti tigawirenso anthu 3.3 miliyoni amene Mvac yatulutsa,” adatero Kalilombe Lachitatu pamene amagawa chimanga m’maboma a Dowa ndi Mchinji.

Pofotokoza mmene ndondomekoyo ikuyendera, Kalilombe adati ntchitoyo yayamba sabata yatha m’maboma a Phalombe ndi Chikwawa.

Iye adati ndondomekoyi yachedwerako chifukwa mndandanda wa oyenera kulandira umachedwa kuperekedwa ku nthambi yawo.

Malinga ndi Kalilombe, sabata ino amayenera kugawa m’boma la Blantyre koma ofesi ya DC yachedwa kupereka mndandanda wa amene akuyenera kulandira.

“Tikufunitsitsa kuti pofika pa 14 mwezi uno tikhale titamaliza. Sitikupereka kwa mafumu koma kwa amene adalembedwayo,” adatero.

Related Articles

Back to top button
Translate »