Chichewa

Kumaona pomvetsera mahedifoni

Listen to this article

Malinga ndi kusintha kwa zipangizo zogwiritsa ntchito, moyo ndi makhalidwe a anthu zikunka zisintha tsiku ndi tsiku.

Pafupifupi aliyense ali ndi foni yam’manja ndipo achinyamata ambiri ali ndi zida zanyimbo zomwe akamayenda amakhala akumvetsera pogwiritsa ntchito mahedifoni.

Kumvetsera nyimbo si chithu cholakwika, kungoti nthawi zina kagwiritsidwe ntchito ka mahedifoni timakhala ngati sitimakaganizira bwino, makamaka tikakhala pamsewu.

Masiku ano umapeza munthu akuyendetsa njinga pakati pa msewu mahedifoni ali kukhutu kotero kuti kaya diraiva wa galimoto aimbe bwanji hutala, wapanjinga samva chifukwa cha nyimbo zomwe akumvetsera.

Madiraiva enanso a minibasi ndi galimoto zina amagundika kukweza nyimbo za mahedifoni ali pamsewu osaganizira kuti akusokoneza ntchito yomwe makutu amayenera kugwira posamala kayendedwe ka pamsewu.

Aliponso ena oyenda pansi omwe akalonga mahedifoni m’mutu amangodziyendera pamsewu mwamgwazo.

Choncho amapezeka kuti akuyenda pakati pa msewu kapena kuoloka nthawi yolakwikwa chonsecho makutu atseka ndipo sakumva chilichonse chochitika pamsewupo.

Khutu ndi chimodzi mwa ziwalo zomwe oyendetsa galimoto komanso oyenda pansi amayenera kugwiritsa ntchito pamsewu kuti amvane, komanso kupewa ngozi ndiye zingathandize kuti azipatsidwa mpata.

Ndi zinthu ngati zimenezi munthu susungulumwa kwenikweni, koma kupanda kusamala nazo zingathe kuchititsa ngozi zomwe zikadatha kupeweka.

Pamsewu pamachitika zinthu zambiri ndipo pamakhala anthu osiyanasiyana-ena amgwazo, ena achangu, ena oledzera. Choncho n’kofunika kuti ukamayendapo nzeru zonse zizikhala pamsewupo mmalo momamvera nyimbo utasiyira ena kuti akusamalire moyo wako.

Matimu 8 mu Presidential Cup

Wolemba

BOBBY KABANGO

M

atimu 8 ndiwo atsala kuti aswane m’ndime ya makotafainolo a mpikisano wa Presidential Cup kutsatira kupambana kwa Nyasa Big Bullets yomwe imathirana wonga ndi Blue Eagles Lachitatu lapitali pabwalo la Nankhaka mumzinda wa Lilongwe.

Awa ndiwo adali masewero omaliza kuti apeze timu ya nambala 8 kutsatira kuchita bwino kwa matimu ena.

Matimu a Mighty Be Forward Wanderers, Moyale, Kabwafu, Epac, Mafco, Dwangwa ndi Max Bullets ndiwo adafika kale m’ndimeyi atachita bwino pamasewero awo.

Nkhondo yolimbirana malo mundimeyi pakati pa apolisi a ku Lilongwe ndi timu ya fuko yak u Blantyre idali ya mtima bii komanso adali masewero ochititsa kaso chifukwa matimu awiriwa ndiwo akhala akuchita bwino m’masewero awo muligi ya TNM.

Matimuwa adalepherana patatha mphindi 90 ndipo woimbira Mabvuto Msimuko adaloza malo aimfa kuti atulutsane kudzera m’mapenate.

Bashir Maunde, Muhammad Sulumba, Chiukepo Msowoya, Yamikani Fodya ndi Pilirani Zonda ndiwo adachinyira Bullets. Mike Mkwate, John Lanjesi ndi McFallen Ngwira a Bullets adaphonya mapenate awo.

Eagles idachinya kudzera mwa Osward Maonga, Gregory Latipo, Victor Nyirenda ndi Gilbert Chirwa, pamene Winster Phiri, John Malidadi, Ackim Kazombo ndi Enock Likoswe adaphonya.

Dolo wa tsikuli adali goloboyi wa Bullets, Ernest Kakhobwe, yemwe adagwira mapenate atatu a Eagles kuphatikizapo yomaliza yomwe adasewera Likoswe, kupangitsa kuti Bullets ifike m’ndime ya makotafainolo.

Lero Dwangwa ilandira Mafco pa Chitowe pamene Epac ituwitsana ndi Moyale pa Civo Stadium.

Tsiku limene Max Bullets iphulitsana ndi Wanderers komanso limene Bullets iphulitsane ndi Kabwafu pakwawo alengezabe mtsogolo muno.

Related Articles

Back to top button