Chichewa

Kumawachenjeza anawa

Listen to this article

 

Ndimakumbuka kuti masiku adzanawo, nkhani zogwiririra anazi zisanafale kwenikweni, mayi wanga ankatikhazika pansi, ine ndi achemwali anga, kutiuza kuti kunjaku kuli anthu ena aupandu omwe amakhoza kuseweretsa matupi a ana n’kuwachita chipongwe.

Apatu nkuti tili achichepere; zaka zathu zili pakati pa zisanu ndi khumi.

Adachenjeza mayi kuti pali ziwalo zina pathupi zomwe munthu wina tisamamulole kuzigwira ndipo adanenetsa kuti wina atakugwira modabwitsa-kaya ndi malume, mlongo wako kapena mphuzitsi-ukuwe, uthawe n’kuwadziwitsa mayi kapena munthu wina wachikulire.

Adachenjezaso kuti aphuzitsi amphongo osazolowerana nawo kusukulu. Adanenetsa kuti aphuzitsi aamuna usakakhale nawo wekha muofesi, kaya m’kalasi ndipo adati akakutuma kuti ukasiye makope kunyumba kapena kuti ukawasesere kunyumbako, uwakanire ndipo akakati wachita mwano adzathana ndi mayiwo.

Adakambaponso za aphuzitsi opereka malikisi ochuluka pomwe mwana walakwa. Adati oterewa tikachenjere nawo chifukwa izi sachita zaulere; amafuna malipiro tsiku lina.

Zomangolandira timphatso ngati switi, bisiketi kaya ndalama kwa anthu osawadziwa bwino adakaniza mayi. Pakhomo ngati pali mnyamata kapena bambo wogwira ntchito, padalinso malire pakachezedwe naye popewa kuti angatikole msampha.

Padali zambiri zomwe mayi ankatilankhula, mwina ankaonjeza kumene, koma adatitsegula maso za kuopsa kwa anthu m’dziko limene timakulamo.

Malangizowa adakhazika m’mitu mwathu kotero kuti sikudali kwapafupi kuti wina atitchere ndale chifukwa mayi adali ataunikira za nzeru zosiyanasiyana zomwe anthu amagwiritsa nthito pofuna kuchita nkhanza kwa ana.

Choncho nthawi zonse ndikamva kapena kuwerenga za mwana amene wagwiriridwa sindilephera kulingalira ngati makolo a mwanayo adayesapo kumuchenjeza za mchitidwewu womwe ukukhala ngati wafalikira m’dziko lathu.

Malangizowa sangagwire ntchito nthawi zonse chifukwa nthawi zina anawa amangokakamizidwa mwadzidzidzi ndi munthu wamphamvu zoti sangalimbane naye.

Komatu kawirikawiri tikumva kuti anthu omwe akugwiririra anawa amawanyengerera ndi switi, ndalama ndi zina zoterozo. Kusonyeza kuti amabwera momuwenderera mwanayu pokambirana naye momupusitsa.

Tikumvanso kuti ana ambiri akugwiriridwa ndi anthu omwe ayandikana nawo; anthu omwe amawakhulupirira ndipo amatha kumupusitsa mwana kuti ayese ngati zomwe akuchita naye n’zoyenerera. n

Related Articles

Back to top button
Translate »