Nkhani

‘Kunyalanyaza kudzetsa ngozi’

Listen to this article

Sabata yangothayi ngozi zidakuta dziko lino pomwe anthu 17 adafa.

Pamene anthu amati akhazikitse mitima pansi, anthu 8 atafa pa ngozi ya basi pamlatho wa Rivirivi ku Ntcheu komanso anthu 4 adamwalira ku Bunda ku Lilongwe ndi 4 kwa Magalasi mumzinda wa Blantyre, Lachisanu kudalinso ngozi ina mumzinda wa Blantyre pomwe munthu mmodzi adamwalira. Ndipo kudalinso ngozi zina ku Zomba, Mzimba ndi Mulanje.

Mneneri wa apolisi James Kadadzera adati ngozi zikuchuluka chifukwa chothamanga kwa madalaivala mosatsata malamulo.

Kadadzera adati madalaivala amakanika kuwongolera galimoto yothamanga kwambiri akadodometsedwa kapena kudzidzimutsidwa pamsewu.

“Mwa zina, ngozi ya galimoto yomwe idanyamula simenti ku Blantyre ndi chifukwa chokanika kumanga mabuleki koma nkhani ndi kuthamanganso kosatsata malamulo. Ukalondoloza zikwangwani za pamsewu, ngozi ikachitika sikhala yoopsa chifukwa munthu amatha kuwongolera komanso kupeweka. Vuto anthu akufuna kukafika msanga atanyamuka mochedwa zomwe zikusokoneza kayendedwe pamsewu,” adatero Kadadzera.

Iye adapempha okwera mabasi kuletsa madalaivala akamayendetsa galimoto mopanda dongosolo.

“Oledzera asaloledwe  kuyendetsa galimoto. Akamathamanga kwambiri chonde dziwitsani apolisi mungakumane nawo kuti adzudzule dalaivalayo. Tili tcheru kuonetsetsa kuti malamulo atsatidwe pamsewu popewa ngozi,” adatero Kadadzera.

Kaamba ka ngozizo, bungwe la akatswiri a zomangamanga la Malawi Institute of Engineers (MIE) ladzipereka kuthandiza apolisi ndi nthambi zonse za boma zoona za pamsewu kuthana ndi ngozi.

Chikalata chosainidwa ndi mkulu wa MIE Martin Chizalema chidati: “Pakuyenera kukhala kafukufuku wozama opeza gwero la kuchuluka kwa ngozi pamsewu. Tiyike mwachangu njira zothana ndi ngozi zoopsazi zomwe zikubwezera chitukuko cha dziko lino m’mbuyo.”

Chizalema adatinso anthu atenge umwini oteteza miyoyo yawo pa msewu komanso eni galimoto azionetsetsa kuti zili bwino komanso kupewa kuimba lamya akuyendetsa. 

Related Articles

Back to top button