Nkhani

Kusakatula manifesito ya MCP

Listen to this article

Loweruka pa 9 March chipani cha MCP chidakhala choyamba kukhazikitsa manifesito ake pokonzekera chisankho chapatatu chomwe chichitike pa May 21.

Chipanicho chakhudza madera onse amene ati chidzasintha ngati chitalowa m’boma.

Oimira MCP: Sidik Mia (kumanzere) ndi Lazarus Chakwera

Akadaulo pa ndale Emily Mkamanga ndi Mustapha Hussein ayamikira manifesitowo ponena kuti ngati atakwaniritsidwa ndiye kuti Malawi atha kudzasintha m’zambiri.

Mkamanga adati: “Ndi manifesito abwino, ngati atalowa m’boma ndi kudzakumbuka zomwe adalonjeza, madera ambiri a dziko lino adzasintha.”

Hussein adati MCP yaluka bwino manifesito ake ndipo chipanicho chiyenera kuwatengera manifesitowo kwa anthu kuti amvetsetse ndi kupanga chisankho.

“Maiko ambiri ngati South Africa mtsogoleri wa dziko amagwiritsira galimoto zochepa akamayenda. MCP ikuti idzagwiritsira ntchito galimoto 10 zokha pamene mtsogoleri akuyenda zomwe ndi zabwino,” adatero Hussein.

Mwa zina, chipanicho chati ndalama yotsikitsitsa yomwe wogwira ntchito adzalandire ndi K50 000. Padakali pano ndalama yotsikitsitsa yomwe anthu akulandira ili pa K25 000.

Manifesitowo akuti boma la MCP silidzadula msonkho kwa amene akulandira malipiro osaposa K100 000. Izi zikusiyana ndi zomwe zili pano chifukwa wodula msonkho amayambira amene akulandira K35 000.

Kumbali ya ulimi, chipani cha MCP chati ndondomeko yomwe dziko lino likugwiritsira ntchito pakagulidwe ka zipangizo zotsika mtengo lidzathetsa.

Icho chati mmalo mwake, chidzatsitsa mtengo wa feteleza dziko lonse kuti aliyense atha kugula mosavuta.

“Njira iyi ndi yabwino, ndipo anthu ambiri adzapindula nayo,” adatero Hussein.

Pofuna kuti alimi azizapindula ndi ulimi wawo, MCP yati ndondomeko ya zachuma izidzayamba m’mwezi wa March osati July monga zilili pano cholinga bungwe la Admarc lizizagula zokolola kwa alimi nthawi yabwino.

Pofuna kuthana ndi katangale, MCP yati idzakhazikitsa khoti lapaderadera lothana ndi ziphuphu komanso katangale lomwe lidzathane ndi nkhani zonse za katangale zomwe zatha zakazaka osakambidwa.

“Palibe chovuta, izi ndizotheka ndipo zikufunika kutero chifukwa milandu yambiri ikuginera m’bwalo lamilandu,” adatero Hussain.

MCP yatinso mtsogoleri wa dziko azidzaonekera kunyumba ya Malamulo komwe azikayankha mafunso amene anthu alinawo. Iyi idzakhala mbiri m’dziko la Malawi chifukwa mtsogoleri amene adapanga izi ndi Bakili Muluzi yekha.

MCP yati idzamanga misewu yamakono komanso boma lililonse lidzakhala ndi malo okwerera mabasi amakono cholinga anthu asamakhale ndi mavuto amayendedwe.

Chipanichi chatinso chidzathana ndi nkhani zamalo poonetsetsa kuti palibe nzika yakunja idzakhale ndi malo.

Manifesito a chipanichi akuti adzaonetsetsa kuti palibe munthu amene adzamwalirire m’chipatala chifukwa cholekereredwa.

Chidzakhazikitsanso National Youth Service (NYS) ndi pologalamu yotchedwa Jobs4Youth yomwe idzasule maluso pakati pa achinyamata.

Chipanichi chatinso chidzayesetsa kuti timu ya ntchemberembaye ya dziko lino ili panambala yoyamba ndipo idzamanga bwalo la timuyi lomwe matimu akunja atha kumadzasewererapo.

Pofuna kuteteza anthu achialubino, chipanichi chidzanyonga aliyense wopezeka wolakwa pa nkhani za alubino.

Chitetezo chawonso chidzakhwimitsidwa m’midzi momwe akukhala komanso komwe akuyenda.

Apolisi akuti azizakhala m’midzi kuti chitetezo chidzakhale chokhwima.

MCP yati idzagwiritsira ntchito galimoto 10 pamene mtsogoleri akuyenda komanso sikudzakhala wapolisi wodikirira kuti mtsogoleri adutse mumsewu.

Hussein wati izi ndizotheka bolani boma lidzakonze malipiro a apolisi chifukwa ambiri amakokera akaima pamsewu kuti mtsogoleri adutse.

Ophunzira amene asankhidwa kusukulu za ukachenjedwe akuti adzapatsidwa kompiyuta.

Related Articles

Back to top button