Chichewa

Kusamala anapiye a mikolongwe

Listen to this article

Amati nkhuku ndi dzira, kusonyeza kuti ngati susamala dzira ndiye kuti udzalandira nkhuku za matenda zomwe sizichedwa kufa. Komanso kupanda kusamalira bwino anapiye, akhonzanso kufa. Koma chisamaliro ichi nchotani? BOBBY KABANGO adakacheza ndi Rose Mphepo, mphunzitsi wa kusukulu ya ziweto ya Mikolongwe m’boma la Chiradzulu. Adacheza motere:

Tidziwane mayi…

Ndine Rose Mphepo. Ndine Assistant Hatchery Manager—wachiwiri kwa woyang’anira malo oswera nkhuku. Koma tikuopeni?

Mphepo kuyang’anira anapiye
Mphepo kuyang’anira anapiye

Tikufuna timve momwe tingasamalire anapiye a mikolongwe.

Kuno tilibe nkhuku mtundu wake mikolongwe. Anthu amangoti nkhuku za mikolongwe, koma palibe mtundu wa mikolongwe. Nkhuku zimenezi ndi ma Black Austrolorp koma chifukwa zimachokera kuno, anthu amangoti mikolongwe. Ndikufotokozerani momwe timasamalira anapiye koma tipite kuofesi kwathuko. Tsono tidaika madzi amene mukaponde musadalowe kuofesiko, madzi amenewo ndi a mankhwala kuti musabweretse matenda kukholako.

 

Chisamaliro cha anapiye amtundu umenewu chimakhala chotani?

Ngati ukufuna kuweta nkhuku zimenezi, choyamba samala mazira. Ndiye tili ndi khola ilo lomwe tikusungako nkhuku 300. Tambala mmodzi ali ndi misoti 10. Zimaikira komweko ndipo mmawa cha m’ma 10 koloko timakatolera mazira komanso madzulo cha m’ma 3 koloko.

 

Mazira amenewa amapita kuti?

Tikatolera, timapita nawo ku hatchery. Iyi ndi nyumba yofungatilitsa mazira kuti anapiye atuluke. Koma tisadawaike m’nyumbayi, timawaika mu Egg Chamber. Awa ndi malo amene timasankhira mazira. Timaikapo zongendawa amene amapha timajeremusi tomwe dzira latenga kuchokera kukhola kuja. Timawasungamo kwa sabata imodzi. Tikawatulutsa m’menemu ndiye timawaika moti akafungatilitsidwe. Dzira ndi chinthu cha moyo, ngati taliyika mu incubator lili ndi majelemusi, ndiye kuti anapiye adzabadwanso ndi matenda. Komanso panthawiyo timasankha mazira amene ali ndi mavuto monga amene ali ang’onoang’ono komanso osweka.

 

Fotokozani zomwe zimachitika mu incubator-mo.

Incubator yathu imalowa mazira 30 000 koma chifukwa cha mavuto ena, sitikwanitsa kuikamo mazira 30 000, mapeto ake timangoika momwe tapezera koma sabata iliyonse Lachiwiri timatulutsa anapiye 4 000. Mavuto enanso nkuti tilibe zakudya zokwanira zosamalira anapiye ngati achuluka. Tikawaika m’menemu, timadikira padutse masiku 18, apa timasankha mazira amene satulutsa anapiye. Dziwani kuti tambala akaphonya pamene akukwera thadzi, dzira limenelo limakhala lakufa loti simutuluka napiye.

 

Zimakhala bwanji kuti Lachinayi lililonse muzitulutsa anapiye?

Nchifukwa choti sitiika mazira 30 000 monga ilili incubator-yi. Ndiye sabata ino timaikamo mazira, ena timaika sabata yotsatira, zomwe zimachititsa kuti anapiye azitulukanso mosiyana. Ena amatha masiku 21 sabata ino pamene ena sabata ya mawa.

 

Kodi anapiye sangapse mmenemu atati atuluka chifukwa cha kutentha?

Kutentha kwa incubator ndi kofanana ndi nkhuku, timaonetsetsa kuti incubator ikutentha madigiri 37.5.

 

Magetsi akazima zimakhala bwanji?

Magetsi akazima mutha kulumikiza jeneleta koma ngati mulibe ndiye azime kwa masiku awiri mutafungatilitsa mazira amene adutsa masiku 18, ndiye mazira onse amaonongeka. Amenewo katayeni chifukwa anapiye amakhala afa.

 

Anapiye akabadwa, mumalowera nawo kuti?

Amabwera m’nyumba iyi. Ndi motentha chifukwa amakhala mwana wathu ali m’chikuta. Kupanda kutentha kumeneku samachedwa kufa chifukwa ndi osakhwima.

 

Katemera mumawapatsa atakula bwanji?

Tsiku lomwe abadwa timapereka katemera woteteza ku matenda. Kenaka timawapatsa madzi ndiye timadikira padutse mphindi 30 tisadawapatse zakudya. Zikatha sabata imodzi, timazipatsa katemera wa gumbolo, sabata yachiwiri timazipatsa katemera wa LaSota, sabata yachitatu timawapatsa gumbolo, yachinayi LaSota, ndipo yachisanu wa firepox. Sabata ya 6 timawagulitsa kwa alimi ndipo mlimi savutika nazo. Alimi amagula K500 mwanapiye mmodzi.

 

Nanga zakudya?

Zakudya timapanga tokha, zikangobadwa kumene mpaka atakula timawapatsa chicken mash.

 

Kodi anapiyewa mumawadziwa kuti uyu ndi tambala, uyu thadzi?

Eya timawadziwa. Tambala amakhala ndi mutu waukulu pamene nkhuku yaikazi imakhala ndi mutu waung’ono.n

Related Articles

Back to top button