Nkhani

Kusamvetsetsana kwabuka ku Mwanza

Listen to this article

Kusamvetsetsana kwabuka pakati pa anthu a ku Mphete m’boma la Mwanza ndi ofesi ya DC wa bomali chifukwa cha nyumba ya mphunzitsi pasukulu ya Mphete imene kampani yokonza njani ya Vale Logistics idagwetsa.

Malinga ndi mlembi wakomiti yoyendetsa ntchito za pasukulu ya Mphete, Allan Gaviyawo , m’chaka cha 2012 a kampani ya Vale Logistics adagwetsa nyumba ya mphunzitsi imodzi pasukulu ya Mphete chifukwa inali pamalo pomwe payenera kudutsa njanji yomwe ikudutsa m’dziko muno kuchokera ku Mozambique.

Gaviyawo adati kampaniyi idalonjeza kuwapatsa anthu a m’derali ndalama zokwana K1.5 miliyoni kuti amangire nyumba ina pamalo ena zomwe anthu a m’derali adakana ponena kuti ndalamayi siinali yokwana kumangira nyumba ina yamakono ngati yomwe inagwetsedwayo yomwe inali mphatso kwa anthu a m’derali kuchokera kubungwe la European Union.

Zitachitika izo, kampaniyo idalonjeza kupereka K12.7 miliyoni yoti nyumba ina imangidwe zomwe anthuwa adagwirizana nazo popeza amayembekezera kuti ndalamayi ikanakwanira kumanga nyumba ziwiri zamakono za amphuzitsi mmalo mwa imodzi.

“Anthu a m’derali anadabwitsika poona kuti ndalamazi zinakapelekedwa kuofesi ya DC yomwe idabwera kudzamanga nyumbayo ndipo anthu aku Mphete sakukhutisidwa ndi nyumba yomwe ofesi ya DC wa boma la Mwanza yamanga pasukulu ya Mphete pakuyerekeza ndi ndalama yomwe idaperekedwa yomangira nyumbayi,” adatero iye.

Wapampando wa khonsolo ya Mwanza Moses Walota adati iye ndi makhansala anzake m’bomali atakayendera nyumbayo adakhumudwa ndi momwe nyumbayo ayimangira ndipo sadakhutisidwe ndimamangidwewo.

Walota wanena kuti ataona izi analembela kalata bwanankubwa wa boma la mwanza yomuunikira zolakwika zomwe mankhansalawa anapeza panyumbayi zoti zikonzedwe nyumbayi isanaperekedwe kwa anthu aku mphete m’mboma la Mwanza. Koma mpaka lero kalatayo siinayankhidwe ndipo zolakwika pa nyumbayo sizinakonzedwebe.

Poyankhapo pankhaniyi DC wa boma la Mwanza Gift Lappozo wavomereza kuti nzoona kuti kontilakitala yemwe adapatsidwa ntchitoyi wayithawa atagwira ntchito yosasangalatsa kumapeto kwenikweni kwantchitoyi koma bwanankubwayu adati padakalipano ofesi yake ikuunikanso bwinobwino mgwirizano omwe anagwirizana ndi kontilakitayu asanapeze wina oti amalizitse ntchitoyi

Koma iye wakana kuti kontilakitayu adapatsidwa ndalama zonse zokhudza ntchitoyi koma kuti amalipidwa m’zigawo akamaliza chigawo chilichonse chantchitoyi moyenerera.

Lapozo adati kusamvetsetsana komwe kulipo pakati pa ofesi yake ndi anthu aku Mphete kwadza chifukwa cha kusadziwa momwe ofesi ya bwanankubwa imachitira pogwira ntchito ngati zimenezi komwe anthuwa alinako ndiponso chifukwa chokuti anthuwosakufuna kumva kufotokoza komwe akhala akufotokzeredwa ndi ofesi ya DC pazankhaniyi.

Related Articles

Back to top button
Translate »