Nkhani

Kusefukira kwa madzi kupha anthu 21

Anthu 21 atsikira kuli chete, pamene ena 100 000 ali kakasi kusowa kopita kutsatira mvula ya mphamvu yomwe yasakaza katundu komanso kusamutsa anthu m’dziko muno.

Izitu zachitika kuyambira mwezi wa July chaka chatha mpaka mwezi uno wa January.

Malinga ndi nthambi ya boma yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), maboma 24 ndi omwe akhudzidwa ndi mavutowo.

Mwa mabomawo, maboma 12 ali m’chigawo cha kummwera 8 chigawo chapakati pamene anayi ali m’chigawo chakumpoto.

Malinga ndi mneneri wa Dodma Chipiliro Khamula, pofika Lamulungu pa 13 January, ngoziyi n’kuti itapha anthu 21.

“Mwa anthuwo, 12 adamwalira ataombedwa ndi mphenzi pamene anthu ovulala pangoziyo adalipo 38,” adatero Khamula.

Iye adati boma lakhala likuwapatsa anthu okhudzidwawo thandizo monga chakudya, zofunda ndowa ndi zina komanso malo okhala mongoyembekezera.

“Ntchitoyo ikupitilira ndipo tikadafikirabe madera omwe ma makhonsolo awo atidziwitsa za ngozi,” adatero Khamula.

Nthambi yoona zakusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (Met), yati kuliraku sikutha chifukwa sabata ino mvula yosefula madzi ikatamuka.

Ena mwa maboma okhudzidwa ndi Nsanje, Karonga, Mulanje, Chikwawa, Balaka ndi Lilongwe.

Polankhula ndi Tamvani, DC wa boma la Mulanje, Charles Makanga adati madzi osefukira ochokera mumtsinje wa Thuchira, Lolemba pa 14 adaononga minda ya anthu 520 ochokera m’midzi ya Kada ndi Nongwe kwa mfumu yaikulu Nkanda.

“Apapa ndiye kuti anthuwo akufunikira thandizo la mbewu ndi zofunikira zina chifukwa minda yawo yakokoloka,” adalongosola Makanga.

Iye adatinso anthu 680 mdera lina komweko ali kakasi mvula ya mphepo itasakaza nyumba zawo.

“Tikuyesetsa kupereka thandizo loyenera kwa anthuwo ngakhale tikudikirabe thandizo lofika kwa anthu omwe ali kakasi ochokera kumsika wa njala komwenso mvula ya mphepo idasakaza katundu,” adalongosola Makanga.

Sabata yathayo, anthu awiri adamwalira m’boma la Balaka ndi wina m’boma la Mangochi chipupa cha nyumba yawo chitawagwera kutsatira mvula yomwe idagwa m’mabomawo.

Ku Mzimba kwa Mberwa, Jalavikuwa, Ntwalo ndi Mabulabo mabanja pafupifupi 1000 akhudziwa ndi mvula ya matalala komanso madzi osefukira.

DC wa bomalo, Thomas Chirwa adati chifukwa choti madera ambiri akhudzidwa pakamodzi, anthu ambiri sadalandirebe thandizo.

Mzinda wa Lilongwe ndi malo enanso omwe madzi adazunguza sabata yatha. Anthu 176 adasamutsidwa ndi madzi ndipo katundu adaonongeka.

Nduna ya zachitetezo m’dziko muno yomwe yakhala ikuyendera anthu okhudzidwawo, Nicholus Dausi idati ngozizo zanyanya chaka chino ndipo mpofunika kuti anthu akhale osamalitsa kukamagwa mvula kapena mphepo.

Nthambi ya Met yapempha anthu kuti azikhala m’nyumba zawo kukamagwa mvula komanso osabisala pansi pa mtengo. n

Related Articles

Back to top button