Chichewa

Kusintha kwa nyengo kwasokoneza ulimi wa khofi

Pamene mlimi aliyense akudandaula ndi kusintha kwa nyengo, nawo alimi a khofi sadasiidwe pamene zadziwika kuti dziko lino likukolola khofi wochepa chifukwa cha kusokonekera kwa nyengo.

Malinga ndi tsamba la pa intaneti la www. mzuzucoffee.org, dziko lino limayembekezereka kumakolola matani 20 000 a khofi koma chifukwa cha kusintha kwa nyengo, dziko lino likungokolola matani 1 500 okha pa chaka.

Kusintha kwa nyengo kwachititsa ulimi wa khofi kulowa pansi
Kusintha kwa nyengo kwachititsa ulimi wa khofi kulowa pansi

Polankhula ndi Uchikumbe, mkulu wa kampani ya Mzuzu Khofi, Harrison Kalua, chaka chino chokha dziko lino likolola matani 1 200 okha a khofi kusiyananso ndi 1 500 amene timayenera kukolola pachaka.

Malinga ndi iye, izi zikusokonezanso kuti ulimiwu usabweretse ndalama zochuluka malinganso ndi kusokonekera kwa ndalama ya dziko lino ya kwacha.

“Alimi a khofi akulira mosalekeza chifukwa chosakhazikika kwa ndalama ya dziko lino,” adatero iye.

Iye adatinso alimi m’dziko muno ali ndi kuthekera kolima khofi wambiri koma vuto ndi kusintha kwa nyengo komwe kukusokoneza ulimiwu zomwenso zachititsa kuti dziko lino lizikolola khofi wochepa.

Malekodi a mwezi wa September amene apanga a Coffee Association of Malawi, akuonetsa kuti dziko lino latumiza kunja makilogalamu 375 800 a khofi mmwezi wokhawu.

Malekodiwa akuti giledi yachiwiri ya khofi wa Floaters ndi Mbuni sadatumizidwe kunja kuti akagulitsidwe.

Alimi amayenera avomereze mitengo yomwe apatsidwa kuti awagulire ngati akhutitsidwa nayo.

Khofi wambiri akulimidwa m’ma esiteti a m’maboma a Thyolo, Mulanje, Zomba, Mangochi. Padakalipano alimi pafupifupi 4 000 ndiwo akulima mbewuyi m’dziko muno ndipo alimiwa ali m’makopaletivi 6.

Makopaletivi ambiri ali m’chigawo chakumpoto komwe kuli Misuku, Phoka Hills, Viphya North, Nkhatabay Highlands, South East Mzimba ndi Ntchisi East komwe alimi 2 500 ndiwo akulima. n

 

 

Related Articles

Back to top button