Monday, April 19, 2021
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Adverts
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa Nkhani

Kutakata ndi ulimi wa mitengo ya zipatso

by ESMIE KOMWA
19/03/2021
in Nkhani
5 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Pamene alimi ena akukangalika ndi ulimi wa ziweto kapena mbewu zina, Pilirani Tendai Khoza adapeza mtaji pa ulimi wa mitengo ya zipatso. Mlimiyu yemwe ndi mwini komanso mkulu wa Phiko Farms m’boma la Lilongwe akufotokoza zambiri za ulimiwu. ESMIE KOMWA adacheza naye motere:

pikho | The Nation Online
Khoza kuonetsa zipatso za mitengoyi

Choyamba mungotidziwitsa kuti phiko farms imapanga chiyani?

RelatedHeadlines

Anthu 49 afa ndi mphenzi

Luso la Joe Kellz mpatali

Tambala walira

Pikho Farms imapanga ulimi wogulitsa mbande za mitengo ya zipatso monga mango, mpesa, mapichesi, malalanje, manachesi, maapulo, mapeyala, mapapaya, ma nectaren, mapulamu, magalagadeya ndi zina zambiri.

Mbewuzi ndi zocha msanga ndipo  zimabereka pasanathe chaka. Ubwino wina wa mitengoyi ndi woti zipatso zake zimakhala zokoma ndi zofewa kusiyana ndi zamakolo.

Nanga  munayamba liti ulimiwu?

Ulimi umenewu ndidayamba m’chaka cha 2012 pamene ndimachita ukachenjede wanga ku Bunda.

Kodi chidakuchititsani kuti muyambe ulimiwu ndi chiyani?

pihko | The Nation Online

Ulimiwu ndidayamba kalekale ndili mwana.

Ndikukumbukira kunyumba ndinali ndi kadimba kuseli kwa nyumba ya kwathu koma nditapita kusekondale ndinasiya.

Ndinakayambiranso nditapita kusukulu ya ukachenjede ndili chaka chachiwiri. Nyengo imeneyo ndi imene  mayi anga adali atamwalira kumene ndipo ndidayamba ulimi wamadimba kuti ndizidzithandizira.

pikho1 | The Nation Online

Ndinayamba kulima ndiwo zamasamba mpaka kukula pano ndimalima mitengo ya zipatso. 

Nanga luso lopanga mbandezi mudalipeza kuti?

Luso limeneli ndidaliphunzira kwa anthu ena malingana ndi chidwi chimene ndinali nacho.

Sindinganene kuti ndinaziphunzira m’kalasi ayi chifukwa lusoli limapezeka  m’pulogalamu  ya ulimi wa zipatso pamene ine ndinachita maphunziro a zankhalango ndi chilengedwe.

Kuyenda m’maiko ambiri ndi kumene kunapangisa kuti ndiphunzire zinthu zambiri zokhudzana ndi ulimiwu.

Nanga mbewu yopangira izi mumaipeza kuti?

Monga ndanena, ndayenda ndithu maiko angapo ku Africa kuno, ku America, ku Mangalande komanso ku Ulaya choncho mbewu ndazitengapo m’maiko osiyanasiyana.

Kodi mbande zanu zimasiyana bwanji ndi za alimi ena?

Choyamba ife mitengo yathu ndi yakolite komaso yambiri ndiyoti ku Malawi kuno kulibe  monga ndanena kale kuti ndatengapo mitengo m’maiko angapo.

Chachiwiri  ife ndi achilungamo pantchito yathu. Mwachitsanzo, munthu tikamuuza kuti uwu ndi mtengo wa  malalanje  zipatso zimakatuluka zomwezo ndithu pamene mavenda ena amakugulitsa mandimu kunama kuti ndi malalanje.

Kuonjezera apo, timapereka ukadaulo mwaulere kwa makasitomala athu mmene angasamalilire mitengoyo chifukwa tili ndi ukadaulo wakuya.

Kodi ulimiwu ndi wopindulitsa?

Ulimi ulionse ngopindulitsa, wasiyana ndi mabizinesi ena chifukwa tsiku lililonse munthu amayenera adye ndiye amayenera kugula ndithu komanso ulimi wa zipatso ku Malawi kuno sitinayambepo.

Tangoganizani kufikira lero tutengabe maapulo ku Joni chonsecho nthaka yathu ndi yolola chilichonse koma  zimangofunikira upangiri wabwino.

Nanga mungafotokoze mwachidule mmene mumapangira mbande zanu?

Mbande zathu timapanga kudzera m’kukwatitsa.

Pali njira zingapo zokwatisira mbande kuti zituluse zipatso zokoma ndi zocha msanga koma zikufunika kalasi yapadera kuti ndilongosole mwachindunji.

Kodi ndi mavuto anji amene mumakumana nawo ku ulimiwu?

Pa ulimi ulionse pamakhala nthawi yoti mwina kugwa zirombo ndi kuononga mbewu ndiye timayenera kuti tipeze mankhwala othana nazo.

Nthawi zina akuba amaba mitengo panazale koma kwambiri vuto limakhala kusowa misika ikuluikulu monga kugulitsa ku boma  zimakanika moti sitidziwa kuti anthu amene amapeza mwayi wotere amatani chifukwa mitengo yathu ndi yabwino komanso yocha msanga.

Vuto lina ndi loti anthu sakuzindikirabe kuti nthaka yathu imalola chilichonse. Mwachitsanzo, tidakaganizabe mwachikale kuti mpesa ku Malawi sachita bwino koma ku South Africa.

Nanga masomphenya anu ndi otani ku ulimiwu?

Ndimafunitsitsa kuti nthawi idzakwane yoti Malawi izidzazilimira zipatso yokha osati ndi ma orange omwe kumatenga m’maiko a eni ayi chonsecho kuthekera tilinako amalawi.

Mawu anu omaliza ndi otani?

Zipatso monga maapulo, mpesa kaya mapulamu ali ndi uthekera kochita bwino m’dziko muno ndipo umboni tili nawo.

Bwerani mudzagule mbande zathu ndipo tidzakuphunzitsani ukadaulo wake kuti mutulutse zipatso zapamwamba zimene zimachokera m’maiko abundance. n

Mukafuna kulumikizana nawo aimbireni foni pa 0888 160 201

Avatar
ESMIE KOMWA
Previous Post

Kunje lawyer dumps case

Next Post

Pirates legend says Gaba is selfish

Related Posts

lightning e1446717884574 | The Nation Online
Nkhani

Anthu 49 afa ndi mphenzi

April 3, 2021
Joe Kellz | The Nation Online
Nkhani

Luso la Joe Kellz mpatali

April 3, 2021
Anthu adaponya voti m’madera ena Lachiwiri
Nkhani

Tambala walira

April 2, 2021
Next Post
Did not make the cut: Gaba

Pirates legend says Gaba is selfish

Discussion about this post

Opinions and Columns

Big Man Wamkulu

Hot babe wants to trap me, should I ran?

April 18, 2021
Political Uncensored

Mighty mess!

April 18, 2021
My Thought

Chakwera’s indecisiveness will be his downfall

April 18, 2021
People’s Tribunal

Cut the crap, act on abuse forthwith

April 17, 2021
https://www.mwnation.com/wp-content/uploads/2021/03/WFP-Afikepo-1-2.pdf https://www.mwnation.com/wp-content/uploads/2021/03/WFP-Afikepo-1-2.pdf https://www.mwnation.com/wp-content/uploads/2021/03/WFP-Afikepo-1-2.pdf

Trending Stories

  • Lilongwe Road | The Nation Online

    OPC frustrates roads projects

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Ministry defends ‘borrowing’ of Covid-19 funds

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Chakwera bites

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Caroline Kautsire: English Professor at Bay State College in Boston

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Chilima in public projects inspection

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2021 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Opinion
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.