Nkhani

Kutentha koonjeza kuzinga maiko

Listen to this article

A nthambi yoona za nyengo m’dziko muno auza Amalawi kuti alimbe mtima chifukwa nyengo yotentha yomwe yakhala m’dziko muno kwa sabata ziwiri zapitazi, kupitirira kwa sabata zikubwerazi.

Kuchokera sabata yatha, dziko lino lakhala likutentha ngati ng’anjo ya moto moti madera a kunsi kwa chigwa cha mtsinje wa Shire kutenthaku kumafika pa 450C pomwe madera ena kumafika pa 350C.

Anthu akhala akudandaula kuti kutenthaku kukusowetsa mtendere.

Zikuoneka kuti nyengo yotenthayi yatikakamira chifukwa a nthambi yoona zanyengo adalengeza Lolemba kuti Amalawi angovala zilimbe chifukwa nyengoyi ipitirira kwa sabata zikubwerazi.

Komatu si dziko lino lokha lomwe lakhaula ndi kutenthaku chifukwa maiko ena ambiri a m’dera la kummwera mu Africa la Southern African Development Community (Sadc) monga Botswana, Eswathini, Mozambique ndi ena.

Malinga ndi kalata yomwe idatulutsa nthambi yoona za nyengo m’bungwe la Sadc Lolemba pa October 28, yachenjeza anthu kuti kutentha molapitsa m’maiko a m’derali.

Pomwe kalata yochokera ku nthambi yoona za nyengo m’dziko muno ya Climate Change and Meteorological Services yomwe adatulutsa ndi mkulu wa nthambiyo Jolamu Nkhokwe idalongosola kuti kuchokera Lamulungu pa October 27 kufika pa November 3, kutentha ndi dzuwa kupitirira.

Kalatayo yati sabata yapitayi madera monga Lengwe National Park m’boma la Chikwawa kudatentha 45˚C pomwe ku Mwanza ndi Nsanje kudafika 44˚C.

“Koma kuchokera Lachitatu pa November 30, mitambo iyamba kumangana m’madera ena a dziko lino zomwe zikhonza kubweretsa mvula ya mphepo ya mkuntho komanso ziphaliwali,” ikutero kalatayi.

Malinga ndi Nkhokwe aka si koyamba kuti m’dziko muno mutenthe chonchi maka m’madera a kunsi kwa chigwa cha mtsinje wa Shire koma kuti chaka chino ndi dziko lonse lomwe latentha.

Nkhokwe adati ana ndi anthu achikulire ngofunika chisamaliro kwambiri pa nthawiyi.

Katswiri pa nkhani za sayansi, chilengedwe yemwenso amadziwa bwino za kusintha kwa nyengo, Professor Sosten Chiotha adati kutenthaku ndi zina mwa zizindikiro za kusintha kwa nyengo.

“Timadziwa kuti timakhala ndi nyengo zosiyana nthawi ndi nthawi ndipo ndi mmene zikuyenera kukhalira, koma kusinthaku  kukakhala kowonjeza kuposa mmene zikuyenera kukhalira, zimalowa m’gulu la kusintha kwa nyengo,” adalongosola Chiotha.

Koma iye adalongosolanso mwachindunji kuti nyengo ikangosintha kamodzi sikusintha kwa nyengo koma kusinthaku kumayenera kukhale kwa nthawi yaitali.

Malinga ndi Chiotha, malipoti a zanyengo m’dziko muno akuonetsa kuti kusinthaku kwakhala kukuchitika kwa nthawi yaitali ndithu.

Naye bwanamkubwa wa m’boma la Karonga, Frank Kalilombe adati bomalinso kwakhala kukutentha molapitsa kuchokera sabata yapitayi.

Iye adati mpofunika kupeza njira zoti ana ndi achikulire adziwe zoyenera kuchita panthawiyi poopa ngozi zodza mwadzidzidzi monga kukomoka ndi zina kaamba ka kutenthaku.

Related Articles

Back to top button