Chichewa

Kuthamanga kwa magazi nkopeweka

Listen to this article

 

Kuthamanga kwa magazi ndi amodzi mwa matenda omwe amatenga miyoyo ya anthu mwadzidzidzi. Kwa nthawi yaitali anthu akhala akuganiza kuti matendawa amagwira anthu olemera okhaokha, anamadya bwino komanso onenepa.

Koma malingana ndi kufotokoza kwa dotolo wa nthendayi kuchipatala cha Kamuzu Central mumzinda wa Lilongwe, a Dr Lumbani Munthali, matendawa akhoza kugwira munthu aliyense ngakhale kuti onenepa ndiwo amakhala ndi pachiopsezo chokulirapo kudwala nthendayi.

Kusuta fodya kukhoza kudzetsa nthenda ya kuthamanga kwa magazi
Kusuta fodya kukhoza kudzetsa nthenda ya kuthamanga kwa magazi

A Munthali adati: “Nthenda ya kuthamanga kwa magazi imayamba kaamba ka zifukwa zosiyanasiyana. Thupi lili ndi mitsempha yomwe magazi amadutsamo kotero mitsemphayi ikaphinjika ndi kuchepa, zimachititsa kuti magazi ayambe kuyenda mothamanga.”

A Munthali adati ngakhale anthu amene amadwala nthendayi popanda chifukwa chenicheni, anthu ambiri amagwidwa ndi nthendayi kaamba kosuta fodya, kumwa mowa, kuyamwira ku mtundu, kusachita majowajowa, kudya zakudya zamafuta komanso za mchere wambiri.

“Mitsempha ya munthu amene sachita masewera olimbitsa thupi siyitakasuka moti magazi amathamanga kwambiri. Anthu ena amadwala nthendayi ngati ku mtundu kwawo wina anadwalapo nthenda ngati yomweyi. Masiku ano anthu ambiri akukhala moyo wapamwamba ndipo zakudya zawo ndi zamafuta kwambiri komanso anthuwo nthawi zambiri amayenda chokhala ndipo sagwira ntchito zolemetsa. Izi zikuchititsa kuti azikhala pachiopsezo chachikulu chogwidwa ndi nthendayi,” adatero a Munthali.

Mmodzi mwa anthu omwe akudwala nthendayi ndipo amalandira thandizo la mankhwala pachipatala cha Kamuzu Central, a Felix Gondwe, adati amakhulupirira kuti thendayi idawagwira mchaka cha 1981 kaamba koti adalekerera thupi lawo ndipo sankachita majowajowa.

“Ndidalibe galimoto koma nthawi zonse ndinkakwera nawo galimoto ya mnzanga. Sindinkachita majowajowa alionse kuti ndilimbitse thupi langa. Ndidanenepa kwambiri ndipo m’chaka cha 1981 ndidapezeka ndi nthenda ya kuthamanga magazi,”adatero a Gondwe womwe amakhala ku Area 36 mu mzinda wa Lilongwe.

Ngakhale kuti nthendayi ilibe zizindikiro zikuluzikulu, a Munthali adati munthu yemwe ali ndi nthendayi amamva kupweteka kwa mutu, chizungulire, kuthamanga kwa mtima, komanso saona bwinobwino.

A Munthali adati munthu akafika kuchipatala kudzapimidwa ngati ali ndi nthendayi, iwo amamuyeza ipso komanso mtima kuti adziwe ngati ziwalozi zikugwira bwino ntchito. Iwo adati munthu yemwe ali ndi nthendayi ziwalo zimenezi sizigwira bwino ntchito zomwe zimachititsa kuti munthuyo azikanika kukodza komanso amakodza pang’onopang’ono

Related Articles

Back to top button
Translate »