Chichewa

Kuthana ndi vuto

Listen to this article

Kwa zaka 20, gulu la alimi a ng’ombe za mkaka la Namahoya la m’boma la Thyolo silimapeza phindu m’nyengo ya mvula chifukwa  limangogulitsa mkaka wokwana magawo 10 pa 100 aliwonse nthawi zina osagulitsa ndikomwe.

Wapampando wa gulili Taulo Chisoso adati izi zimachitika chifukwa ogula akayeza mkaka umaupeza uli ndi madzi wochuluka.

Wyson kudyetsera udzu ng’ombe yake

Koma padakali pano, mkuluyu adati vutoli adathana nalo.

“Kwa zaka zonsezi, nyengo ya mvula ikafika kwambiri tinkangodyetsera udzu wauwisi chifukwa umapezeka wochuluka osadziwa kuti tikuzionongera msika,” adatero Chisoso yemwe gulu lake lili ndi mamembala 550.

“Mu 2016 tidapeza ulangizi woti kudyetsera kwambiri ng’ombe za mkaka msipu wobiriwira, kumachulukitsa madzi ku mkaka ndipo titaleka, taona kuti chaka chonse chatha mpaka lero sudabwererepo pamsika,” adatero Chisoso.

Mlimiyu adati kampani yomwe imawagula, imafuna mkaka wabatala loyambira magawo 20 pa 100 aliwonse.

Akalephera kukwaniritsa izi, amaubweza.

Membala wa gululi, Chrissie Wyton, adati m’mbuyomu nyengo ya mvula ikafika amadyesera msipu wauwisi wabwiri chifukwa deya amakwera mtengo, komanso samapanga mfutso wa ziweto.

“Padakali pano, ndidaleka kudyetsera udzu wauwisi wochuluka chifukwa ndimapanga mfutso pophatikiza msipu wa mitundu yosiyanasiyana kuti zikamadya, zizipeza michere yokwanira m’thupi.

“Kuonjezera apa, ndimasunga madeya chifukwa ndazindikira kuti ulimiwu ndi bizinesi choncho ndikuyenera kumaikirapo mtima,” iye adatero.

Mlangizi wa ziweto ku Mzuzu Agriculture Development Division (Mzaad), Jacob Mwasinga, adafotokoza kuti kudyetsera kwambiri ng’ombe za mkaka msipu wa uwisi kumakhala ngati mlimi akuzipatsa madzi ambiri, koma chakudya chochepa.

“Izi zili chomwechi chifukwa msipuwu, umangochuluka madzi, koma michere imachepa.

“Mkaka umakhala wochuluka, koma ngakhale kungouyang’ana, umaoneka ngati wathiridwa madzi choncho sungayembekezere zabwino pamsika,” iye adatero.

Mwasinga adafotokoza kuti udzu umakhala ndi michere yochulukirapo mapeto a mwezi wa February kapena mayambiriro March.

Iye adati izi zili chomwechi chifukwa umakhala wakula ndipo ukupita kokhwima kotero umakhala ndi michere yochulukirapo.

Mlangiziyu adati ichi n’chifukwa chake alimi amayenera kupanga mfutso wa ziweto udzu ukafika pamenepa.

Pothirirapo ndemanga, mphunzitsi wa ziweto wa ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), Jonathan Tanganyika, adati ngakhale msipu ndi wodalirika pa ulimi wa ziweto, alimi azichulutsa chakudya choonjezera mu nyengo ya mvula.

“Zakudya zoonjezerazi ndi monga madeya, koma kwa alimi omwe ali ndikuthekera, akhoza kumakagula chakudya cha ng’ombe za mkaka chakasakaniza ku sitolo.

“Kuonjezera apa, akhoza kupanga okha posakaniza zinthu zomwe ali nazo monga chimanga, soya kapena nandolo,” iye adatero.

Ngakhale izi zili chomwechi, Tanganyika adati maso a alimi asakhale pakupeza mkaka wokhathamira kwambiri  kuopa kuzichepetsera phindu. n

Related Articles

Back to top button