Chichewa

Kutumiza ana kundende si yankho—Jaji

 

Jaji wa kubwalo lalikulu (High Court) Justice Annabel Mtalimanja wati kuthamangira kugamula ana achichepere kukagwira ukaidi kundende ndi njira imodzi yopititsira uchigawenga patsogolo.

Mtalimanja adalakhula izi posachedwapa poyamikira ntchito yomwe likugwira bungwe losamala ana ndi kuwaphunzitsa zachikhalidwe chabwino la Chisomo Children’s Club.

Mtalimanja: Ana asapite kundende  za akulu
Mtalimanja: Ana asapite kundende
za akulu

Mtalimanja adati ana achichepere akapita kundende amakakumanako ndi anamandwa pazauchigawenga omwe amawagawira nzeru zolakwika ndipo akatuluka amakayeserera zomwe adaphunzirazo moyo wauchigawenga n’kupitirira.

“N’koyenera kwake kuti munthu yemwe walakwira lamulo alandire chilango koma mpofunika kuunika bwino kuti kodi chilango chomwe chikuperekedwacho zotsatira zake zikhala zotani chifukwa cholinga cha chilango n’kuwongola, koma nthawi zina kumatheka kukhotetserakhotetsera.

“Chomwe ndikutanthauza apa n’chakuti chilango chomwe chikuperekedwa chizifanana ndi msinkhu wa munthu wolangidwayo. Ana achichepere, mwachitsanzo, akhoza kuongoka polandira maphunziro achikhalidwe chabwino,” adatero Mtalimanja.

Bungwe la Chisomo Children’s Club lidayambitsa pologalamu ya Mwayi Wosinthika yomwe amaphunzitsa achinyamata opezeka olakwa za mmene angasinthire moyo wawo ndi kukhala achinyamata odalirika.

Mkulu wa bungweli Charles Gwengwe adati pakalipano bungweli laphunzitsapo achinyamata ochuluka ndipo pano ena adasinthiratu moti akugwira ntchito, ena akuchita bizinesi ndipo ena adabwerera kusukulu.

“Sitiphunzitsa zakusukulu, ayi koma mmene munthu angakhalire ngati munthu pakati pa anzake. Ambiri mwa ana omwe timaphunzitsa amakhala ndi milandu ing’onoing’ono monga kupezeka malo olakwika ngati omwera mowa, kuchita mchitidwe woyendayenda ndi kuba pakhomo pa makolo awo.

“Timayenda m’malo oweruzira milandu, m’ndende, ndi kupolisi kusakasaka ana a milanduyi ndipo tikawapeza timapanga dongosolo lowatenga kuti tikawaongole,” adatero Gwengwe.

Pologalamuyi imayenda ndi thandizo lochokera ku Ireland kudzera mu nthambi yolimbikitsa njira zina za kaweruzidwe ka milandu yomwe imatchedwa kuti mpatutso (Diversion Program).

Related Articles

Back to top button