Chichewa

Kuvulaza namfedwa

Listen to this article

 

Ndinali pa maliro ena masiku apitawa komwe amfumu adaganiza zokhutula nkhawa zawo za anamfedwa tili kumanda. Amfumuwo adati sadakondwe ndi momwe bambo wa malemu ankathamangira thamangira pamaliro mmalo mosiira ena kuti amuthandize.

Polankhula, amfumuwa adadzudzula bamboyo akuti chifukwa ali ndi chizolowezi chochita zinthu mwayekha posafuna kuthandizidwa ndi ena. Aka sikanali koyamba kumva anamfedwa akudzudzulidwa mokhadzula mokhudzana khalidwe lawo pamudzi.

Ena amadzudzulidwa kaamba kosapezeka maliro akagwera anthu ena. Ena amadzudzulidwa chifukwa chophonya ndondomeko kapena miyambo ina yokhudza maliro. Ndaonaponso anamfedwa ena ataphikiridwa nsima pamaliro nkuwasiira kuti adye okha ati chifukwa iwo akapita kumaliro a ena sadya chakudya.

Pamene anthu tikukhala m’magulu, sipangalephere wina kulakwitsa kapena kulakwira ena. Nthawi zina pa zifukwa zomwe sitidziwa ena sachita nawo zoyembekezeka pagulu ngati kudya nsima pamaliro. Osakhala kuti akudana ndi nsimayo koma anthufe timayenda ndi matenda osiyanasiyana omwe nthawi zina salola ena kumangodyapo chisawawa.

Ena kungodya za mchere kaya mafuta ndiye kuti aputa zosaputa m’thupi. Sangakwanitse kulengeza za matenda awo kwa aliyense kuti awamvetsetse, nthawi zina kachetechete amangopewa zakudya zomwe sizinaphikidwe mwa dongosolo lomwe adapatsidwa kuchipatala.

Yakhota pang’ono nkhaniyi, apa pagona nkhani lero ndi pa funso ili kuti nchi chifukwa chiyani amfumu ngakhalenso atsogoleri a m’madera ndi midzi yomwe tikukhala amafuna kumudzudzula namfedwa panthawi imene akumva kale kupweteka kotaya mbale wake? Amene mwaferedwapo mukudziwa kuwawa kwa imfa.

Tsopano munthu wa bambo akuika mwana wake m’manda, koma mfumu nkuimilira pamzinda wa anthu nkumamuloza chala bamboyu kumamuuza kuti azitha kukhala pansi kuti ena amuthadize? Nkuthekadi bamboyu adali ndi vuto, koma nthawi yomudzudzula nkumamuchititsa manyazi ikhale imeneyi chitanda cha mwana wake chili poteropo?

Kudzudzula mayi amene sagona kumaliro anzake zikawaonekera nkofunika, koma kodi nthawi yoyenelera kuchita izi ndi yomwe mayiyu akulira mwamuna kapena mwana wake? Mumatani kumudzudzula munthu uja kuseli komanso nthawi yoti kwawo kulibe maliro?

Pamenepa ndikuona ngati atsogoleri athu pamawakanika. Munthu opsinjika ndi imfa tisamupsinjenso ndi zina kufikira chipsinjochi chitapepuka ndiye tikhoza kutsekula pakamwa pathu nkumakamba nkhani zinazi. Nthawi yomwe wina akulira ena tisachenjerepo kumasaka mwayi oti tioneke anzeru pomuvulaza munthu oferedwa ndi mau owawa. n

Related Articles

Back to top button