Chichewa

Kuweta ng’ombe zamkaka nkokoma, koma….

 

Alimi ndi akadaulo ena pa zaulimi abwekera ubwino ndi phindu la ulimi wa ng’ombe, koma ati pali zina zoyenera kuchita kuti ulimiwu ufikepo. Mwa zina, ngakhale alimi ambiri amene adacheza ndi Uchikumbe m’zigawo zonse za dziko lino adati akusimba lokoma paulimiwu pali zina zoyenera kukonza kuti phindulo libwere pambalambanda. Kadaulo pa nkhani ya ziweto kusukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) pulofesa Timothy Gondwe komanso mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi ulimi la Civil Society Agriculture Network (CisaNet) a Tamani Nkhono-Mvula adaphera mphongo zonena za alimiwo.

A Gondwe adati pakadalipano alimi a ng’ombe zamkaka akuchuluka koma chiwerengero cha ng’ombe nchochepa.

Pali zina zoyenera kusintha kuti alimi a mkaka apindule kwambiri
Pali zina zoyenera kusintha kuti alimi a mkaka apindule kwambiri

Iye adati izi zili choncho chifukwa ambiri mwa iwo ndi ang’onoang’ono ndipo amakhala ndi ng’ombe imodzi kapena ziwiri.

“Alimi akuluakulu sakuonetsa chidwi ndi ulimiwu. Alimi aang’ono ambiri alibe zipangizo komanso akusowa ulangizi pa kadyetsedwe, kasamalidwe ka ng’ombe komanso momwe angasamalire mkaka wawo kuti ukapeze msika wabwino,” adatero Gondwe.

Adapereka chitsanzo cha ng’ombe ya mkaka ya mtundu wa Fresian imene itadyetsedwa bwino ikhoza kutulutsa malita 40 pa tsiku koma alimi ambiri amakama malita 10 kapena 12 okha patsiku.

Iwo adatinso vuto lina ndi ndondomeko zoyendetsera msika wa mkaka.

Pophera mphongo, Nkhono-Mvula adati imodzi mwa ndondomeko zimene zimathimba alimiwa pakhosi ndi Gawo 36 ya malamulo a bizinesi ya mkaka.

“Malingana ndi lamuloli, alimi ang’onoang’ono sangagulitse mkaka wawo momasuka pokhapokha atakhala ndi njira zowiritsira yomwe ndi ntchito ina yapadera chifukwa afuna kudutsa m’ndondomeko zambiri kuti avomerezedwe kutero.

“Pachifukwa ichi, alimiwa amakakamizidwa kukagulitsa mkaka wawo kumakampani omwe ali ndi zipangizo pamtengo wozizira,” adatero iwo.

Malinga ndi mkuluyo, alimi a mkaka ali pachipsinjo cha misonkho kusiyana ndi alimi ena poti iwo amadulidwa msonkho pa ndalama zilizonse zomwe angapate pa malonda awo pomwe pamalamulo a msonkho, munthu amayenera kudulidwa msonkho ngati wapeza ndalama zoposa K50 000 pa mwezi.

Mawu a akadaulowa akungopherezera zimene alimi ena m’zigawo zonse zitatu adauza Uchikumbe.

Wapampando wa gulu la Lusangazi Dairy Farmers Cooperative ku Mzimba, Hesco Banda, adati vuto la kusowa kwa zakudya likuchititsa miyoyo ya alimiwa kukhala yowawa. Iye adati ngakhale alimi ali ndi kuthekera kogula chakudya cha ng’ombezo pamtengo wa K10 000 thumba la makilogalamu 50, chikusowa.

“Zakudya zikusowa, moti tikungogwiritsa ntchito deya. Vuto lake,

deyayu tikulimbirananso ndi anzathu a ku Tanzania amene akulolera kugula deyayo pamtengo wa K500 pa kilo mmalo mwa mtengo wake wa K200,” adandaula Banda.

Vuto lina, iye adati, ndi kusowa kwa msika chifukwa kumpoto kulibe

kampani zogula mkaka monga momwe zilili m’zigawo zina. Kampani za Lilongwe Dairy, Suncrest Creameries komanso Dairibord zimagula mkaka kumwera ndi pakati. Adaonjeza kuti izi zachititsa kuti mavenda alowererepo, pomagula mkaka pamtengo wolira.

Ngakhale msika ulipo, alimi ena, monga Thomson Jumbe wa m’mudzi mwa Waruna, T/A Chimaliro ku Thyolo mitengo ndiyotsika. Malingana ndi unduna wa malimidwe, mtengo wotsikitsitsa umene mkaka uyenera kugulitsidwira ndi K155 pa lita.

“Timagulitsa mkaka pa mtengo wa K150 pa lita pomwe kuti titulutse lita imodzi zimalowa ndi zambiri, makamaka tikawerengera zakudya monga deya komanso mankhwala,” adatero Jumbe.

Poyankhapo pamadandaulowa, nduna ya zamalimidwe ulimi wothirira ndi chitukuko cha madzi Dr George Chaponda adati unduna wake uunika madandaulowa nkuwona kuti ungathandizane bwanji ndi alimiwa kuti ulimiwu upite patsogolo.

Related Articles

Back to top button