Chichewa

kwa Ng’ombe zamkaka zimalira chisamaliro chokwanira

Listen to this article

Lasford Mbwana ndi mmodzi mwa alimi a ng’ombe zamkaka omwe akuchita bwino kwambiri kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo. Moti mlimiyu akuyenda chokhala kaamba koti adagula galimoto kuchokera mu ulimiwu. BRIGHT KUMWENDA adacheza naye motere:

Tafotokozani, kodi ulimi wa ng’ombe zamkaka mudayamba liti?

Ulimi wa ng’ombe zamkaka ndidayamba 2006 nditaona momwe anzanga amapindulira. Moti ng’ombe yanga yoyamba ndidagula K130 000 ndipo ndakhala ndikuonjezera mpaka zidafika 8.

Kodi mwapindula motani ndi ulimiwu?

Mbwana kudyetsa ngombe zake zizipereka nkaka wochuluka
Mbwana kudyetsa ngombe zake zizipereka nkaka wochuluka

Phindu ndi losachita kunena. Ndikadakhala kuti sindikupindula sindikadaonjezera chiwerengero cha ng’ombe zanga. Ng’ombe za mkaka zimandipatsa ndowe zothira kumunda, ndalama zogulira chakudya, zovala ndi zinthu zina zosoweka pabanja panga. Panopa banja langa likuyenda chokhala chifukwa choti tidagula galimoto kuchokera mu ulimi womwewu.

Nanga mungamulangize zotani munthu amene akufuna kuyamba ulimi wa ng’ombe zamkaka?

Choyamba akhale ndi ndi chidwi ndi ziweto, malo wobzala nsenjere, amange khola labwino, akhale pafupi ndi madzi, komanso msika wa mkaka.

Kodi mukati khola labwino mukufuna kunena chiyani?

Khola labwino limakhala ndi malo wodyera, wokamira mkaka, womwetsera mankhwala, wosewerera, wokhalira mwana akabadwa, woti ng’ombe izikhala panthunzi ikafuna kupuma kapena kugona.

Kodi patsiku mumakama mkaka wochuluka motani?

Ngakhale ndili ndi ng’ombe 8 ndikukama zinayi zokha chifukwa choti zina ndi zazing’ono. Udzu, deya ndi masese zikamapezeka mosavuta ndimakama malita osachepera 100 patsiku omwe amandipatsa ndalama zokwana pafupifupi K500 000 pamwezi.

Chinsinsi choti ng’ombe izitulutsa mkaka wambiri n’chiyani?

Kudyetsa mokwanira, komanso mtundu wa ng’ombezo. Ng’ombe sizisiyana ndi munthu. Kodi simukudziwa kuti mayi akamadya mokwanira mwana wake amasangalala chifukwa choti mkaka umatuluka wambiri? Ng’ombe zamakono zimatulutsa mkaka wambiri pofanizira ndi ‘zachikaladi’.

Mukati ng’ombe ‘zachikaladi’ mukufuna kutanthauzanji?

Ukapereka umuna wa ng’ombe za Chizungu kwa ng’ombe zachikuda za Malawi Zebu, ana obadwa amakhala makaladi—sakhala azungu kapena achikuda. Amakhala a pakatikati. Moti mkaka omwe amatulutsa sukhala wambiri ngati wa ng’ombe ya Chizungu, komanso sukhala wochepa kwambiri ngati wa yachikuda.

Kodi ng’ombe zanu ndi za mtundu wanji?

Ng’ombe zanga ndi za mtundu wa Holstein. Alimi ambiri a ngo’mbe za mkaka m’dziko muno akuweta ma Holstein, Jersey kapena ma Friesian.

Tafotokozani, kodi mumagula kuti ng’ombe zamkaka?

Timagula kwa alimi anzathu. Ena amagula m’mafamu a boma monga ku Mikolongwe ku Chiradzulu, Likasi ku Mchinji, Diamphwi ndi Dzalanyama ku Lilongwe ndi Dwambadzi ku Mzimba. Mabungwe a alimi a ng’ombe zamkaka a Shire Highlands Milk Producers Association (Shmpa), Central Region Milk Producers Association (Crempa) ndi Mpoto Dairy Farmers Association (MDFA) amathandizanso alimi kupeza ng’ombe zamkaka.

Nanga munthu asungire zingati akafuna kugula ng’ombe zamkaka?

Zimatengera ndi wogulitsa, komanso komwe ukukagula ng’ombezo. Alimi ambiri amagulitsa ng’ombe pamtengo wapakati pa K250 000 ndi K300 000. Ikakhala yabere imafika mpaka K400 000.

Ndi mavuto otani omwe alimi a ng’ombe zamkaka amakumana nawo?

Kusowa kwa madzi ndi zakudya makamaka miyezi ya pakati pa October ndi April. Nthawi imeneyi deya amasowa, komanso udzu umavuta kuwupeza. Moti alimi amayenda mitunda italiitali kuti apeze udzu wodyetsa ng’ombe zawo. Chaka chathachi thumba la deya tim0agula K6 000. Ngakhale adali wokwera mtengo, amavuta kupeza. Kuthimathima kwa magetsi kumawononga mkaka. Alimi a ng’ombe zamkaka amapanga magulu osiyanasiyana (bulking groups) omwe amasunga mkaka wawo m’malo ozizira, kudikira makampani kuti adzagule mkakawo. Magetsi akathima, mkaka ndi kuwonongeka asadadzautenge ndiye kuti alimi ali m’madzi. Kuphatikizira apo, mitengo yomwe makampani amatigulira mkaka ndi yotsika kwambiri. Ulimi wa ng’ombe zamkaka susiyana ndi wa fodya chifukwa wogula ndi amene amayika mtengo.

Ndi matenda otani omwe amagwira ng’ombe?

Chifuwa chachikulu, chigodola, zotupatupa ndi ena mwa matenda omwe amazunza ng’ombe.

Nanga mawu anu otsiriza ndi wotani?

Potsiriza ndikufuna ndipemphe anzanga kuti akumbe zitsime ndi kubzala nsenjere kuti asamavutike kupeza madzi ndi chakudya mudzinja.

Related Articles

Back to top button
Translate »