ChichewaNkhani

Kwaterera kwa ntenje

Listen to this article

 

Mwanunkha m’mudzi mwa Ntenje kwa T/A Machinjiri m’boma la Blantyre komwe osungitsa chitetezo m’midzi (community police) adatibulidwa n’kumangiriridwa pamtengo kumanda komwekonso adawakumbitsa manda.

Kuonjezera apo, apolisi omwe amati akasungitse bata kumeneko adabwerako akulikumba la mtondo wadooka, kuthawa anthu okwiya, malinga ndi Gulupu Ntenje wa deralo.

Mmene timalemba nkhaniyi n’kuti achitetezo a m’mudzimu akubisala m’tchire pamene ena akulandira chithandizo pachipatala cha Limbe.

Akulephera kukhala chifukwa chovulazidwa m’matako: Story
Akulephera kukhala chifukwa chovulazidwa m’matako: Story

Ntenje, yemwe nkhaniyi idachitika m’mudzi mwake, adati izi zidachitika pamene anthuwo amaganizira kuti achitetezowo adapha munthu.

Gulupuyu akuti lidali Lachinayi pa 1 October pamene m’mudzimo anthu ankathamangitsa mnyamata wina amene amamuganizira kuti waba thumba la chimanga kwa agogo ake.

“Anthu adamugwira ndipo adayamba kumumenya. Achitetezo cha m’mudzi ndiwo adamulanditsa kuti asavulazidwe. Adakamutsekera muofesi ndipo adaimbira apolisi ya Bangwe kuti adzamutenge,” adatero Ntenje.

Iye adati pamene nthawi imakwana 4 koloko madzulo, apolisi adali asadafikebe.

“Adatiuza kuti alibe mafuta. Kenaka poti tikamuone munthuyo tidapeza kuti wamwalira,” adatero Ntenje.

Lamulungu pa 4 October, mwambo wa maliro udayamba, koma khamu la anthu am’mudzimo akuti lidayamba kunena kuti a achitetezo a m’mudzi ndiwo adapha malemuyo.

Mmodzi mwa achitetezowo, Davie Story, adati anthuwo adafika kunyumba kwake namugwira cha m’ma 8 koloko mmawa.

“Adandigwira kuphatikizaponso anzanga ena awiri amene timagwira nawo ntchito ya chitetezo cha m’mudzi. Adatitengera kwa wapampando wathu, koma tidakapeza atcheyawo atathawa. Ndiye adatenga mkazi wawo.

“Adatitengera kumanda komwe adatikumbitsa manda. Titamaliza adayamba kutikwapula n’kutimangirira pamtengo,” adatero Story.

Ntenje adati panthawiyo, iye adaimbira apolisi kuti abwere. Apolisiwo akuti adalipo anayi ndipo atafika kumandako anthu okwiyawo adayamba kunola zikwanje kuti athane nawo.

“Zinthu zidavuta, ndipo adaitana apolisi ena. Atafika enawo, tidayesera kukamba ndi anthu okwiyawo kuti awamasule pamtengo achitetezowo, zomwe zidatheka,” adatero Ntenje.

Koma akutsitsira m’manda bokosi la maliro, mphekesera idamveka kuti anthuwo amafuna kuti achitetezowo awaponyere m’dzenjemo n’kuwakwiriria limodzi ndi chitandacho.

Story, amene akukanika kukhala pansi chifukwa cha kuvulazidwa m’matako, adafotokoza malodzawo motere: “Adati tonse anthu 5 tigone limodzi ndi malemuwo. Amati atiponyera m’dzenjemo. Zitavuta, apolisi adayamba kutithawitsira komwe adaimika galimoto yawo.”

Ntenje adati apolisi adathira utsi wokhetsa misozi komabe sizidaphule kanthu ndipo adatha phazi kusiya m’mudzimo muli chipwirikiti.

Apa mpamene anthuwa adapita kukagwetsa ofesi ya achitetezowo komanso kukayatsa nyumba ya wapampando wawo kuphatikizapo nyumba ya Story.

Wapampandoyo, Damiano Dindi, amene adalankhula pafoni ndi Msangulutso kuchokera ku Nsanje, komwe amati akubisala, adati palibe chomwe wapulumutsa m’nyumba mwake.

“Akazi anga ali m’manja mwa apolisi komwe akutetezedwa; mwana wanga wapita kwa achibale; ineyo ndili m’tchire pansi pa mtengo wa bulugama m’boma la Nsanje. Sindikudziwanso kuti ndi m’mudzi mwa ndani,” adatero Dindi.

“Kolowera kwandisowa. Mutu wanga sukugwira chifukwa m’nyumbamo mudali K280 000 ya bizinesi komaso katundu wanga yense wapita.”

Mneneri wa polisi ya Limbe, Pedzisai Zembeneko, adatsimikizira Msangulutso za nkhaniyi ndipo adati womwalirayo dzina lake adali Nyadani Dankeni.

Koma Zembeneko adati kafukufuku pankhaniyi adali mkati ndipo adzalankhula zambiri akamaliza zofufuza zawo.

Pakalipano palibe amene wamangidwa kaamba ka kumwalira mwadzidzidzi kwa Dankeni kapena, adatero mneneri wa polisiyu.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »