Nkhani

Lamulo latsopano la zipani alikambirana

Listen to this article

Dziko lino lili ndi zipani zoposa 40. Komatu mwa zipanizi zisanu zokha ndi zomwe zimakangalika pomwe zina zili ziii ngati madzi a m’filiji kudikira nthawi ya zisankho. Komatu mchitidwewu ukhala mbiri yakale malinga ndi lamulo latsopano la zipani lomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo akuyembekezera kukambirana akakumananso mwezi wa May.

Malinga ndi mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo, Kondwani Nankhumwa, aphungu adzakambirana za lamuloli mwezi wa May chifukwa pamene aphungu akukumana panopa, nthawi ndi yochepa.

Kupereka ndalama, zinthu zina kwa ovota kudzaletsedwa

“Tikadakonda tikadakambirana za lamuloli koma nthawi yangochita njiru. Imeneyi ilowanso pamndandanda wa zokambirana za mwezi wa May,” adatero Nankhumwa.

Ndi lamuloli, zipani zizikakamizika kuonetsa kuti zikugwira ntchito yake, monga kupanga nawo zisankho, komanso kupanga misonkhano yaikulu ya mamembala m’chipani ndi cholinga choonetsa kuti zikugwiradi ntchito zotumikira anthu.

Zikapanda kukwaniritsa izi, mpamene mkulu woyang’anira zipani azizichotsa m’kaundula.

Lamulo latsopanolo lidzachotsa lamulo lakale la zipani lomwe limaona kulembetsa kwa chipani ndi ndondomeko zotsatira.

Mwa zina, lamulo latsopanolo lomwe lili ndi magawo 8 likuunikira zingapo, monga kukhazikitsa ofesi ya wolembetsa ndi kuthetsa zipani, zipani kulongosola bwino momwe zimapezera ndalama komanso kuti mamembala azidziwa momwe ndalama za chipani zikuyendera.

Lamulolo likutambasulanso za kayendetsedwe ka zisankho monga  kuthana ndi mchitidwe wopereka ndalama ndi zinthu zina kwa ovota nthawi ya chisankho komanso kukhala membala wa zipani zingapo.

Polankhulapo za kufunika kwa lamuloli, mkulu wa bungwe limene muli zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD), Kizito Tenthani adati adati padakalipano mamembala a zipani alibe mphamvu zenizeni m’zipani mwawo, zimene lamulolo likufuna kusintha.

Bungwelo ndi  lomwe lakhala likukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa momwe lamulolo lidzathandizire zipani kukwaniritsa ntchito yoimirira anthu komanso kupereka umwini wa chipani kwa mamembala.

“Zimaoneka ngati atsogoleri ndi amene amakhala ndi mphamvu zambiri m’chipani. Lamololi lithandiza kusintha zimenezi. Kuonjezera apo, ndale zathu M’malawi muno zakhala   kwambiri zodalira ndalama. Panthawi ya chisankho, zipani, komanso amene akufuna kuimira zipani pamipando yosiyanasiyana amakhala akupereka ndalama ndi zinthu zina n’cholinga chokopa anthu kuti awavotere,” adatero Tenthani.

Iye adati mchitidwewu umapangitsa ndale kukhala zodula, komanso anthu omwe ali ndi ndalama kukhala ndi mwayi wolowa m’maudindo ngakhale nthawi zina anthu oterowo amakhala opanda masomphenya a mmene angathandizire anthu kudera kwawo.

“Lamuloli lithandiza kuthetsa mchitidwe umenewu. Likufunanso zipani zandale zizinena komwe zimapeza ndalama n’cholinga chothetsa mchitidwe wa katangale,” adaonjezera Tenthani.

Koma mmodzi mwa akadaulo pa ndale m’dziko muno Rafiq Hajat adati palibe chaphindu chomwe lamulo latsopanolo liphule chifukwa lamulo lomwe lilipo lakanika kugwiritsidwa ntchito bwino.

Hajat adati mwachitsanzo lamulo lakaleli limati chipani chilichonse chizipereka kwa mkulu wakalembera wa zipani momwe achitira pa chuma chaka chikamatha ndipo kuti ngati satero chipanicho chizithetsedwa.

“Komatu izi sizili choncho. Ngati tikukanika kukwaniritsa zinthu ngati izi, ndiye lamulo latsopanoli tidzaligwiritsa ntchito bwanji?” adadabwa Hajat.

Iye adati aphungu ayenera kutenga nthawi yaitali kukambirana zinthu monga za kuba ndalama m’boma (cashgate), njala ndi zina osati za lamulo la zipanili.

“Tiyeni tiyang’ane njira zogwiritsa ntchito lamulo lakale lomweli,” adatero Hajat.

Komatu Tenthani adatsutsa izi polongosola kuti lamuloli ndi losiyana kwambiri ndi lakaleli chifukwa layesera kukonza zimenezi ndipo akukhulupilira kuti lidzagwiritsidwa ntchito bwino.

“Choti anthu adziwe n’chakuti lamulo lilipo pano lidapangidwa mwachangu kwambiri n’cholinga choti m’chaka cha 1993 anthu athe kulembetsa zipani kuti zikapange nawo chisankho cha 1994.  Mmalo ambiri, lamulo lili panoli silinaunike bwino maka pankhani ya kayendetsedwe ka zipani, komanso kuumiriza kuti zipanizo zitsatire malamulowo,” adalongosola Tenthani.

Related Articles

Back to top button