Nkhani

Lero moto, mawa moto!

Listen to this article

Pali mtunda kuti dziko lino likhale lodzidalira pothana ndi ngozi zamoto pamene zadziwika kuti makhonsolo m’dziko muno alibe zipangizo zokwanira kuthana ndi ngozizi. 

Komwe kuli vuto kwambiri ndi m’maboma komanso kumudzi komwe kulibiretu zipangizozi ndipo anthu akugwidwa njakata moto ukabuka.

Kampani ya Leopard Matches idabuka moto Lolemba

Izitu zikuchitika pamene ngozi zamoto zafika ponyanyira m’dziko muno. Pafupifupi tsiku lililonse kukumamveka nkhani yoti kwina kwapsa.

M’sabatayi nyumba ya woimira boma pa milandu Kalekeni Kaphale idayaka moto ku Blantyre Lamulungu. Ndipo Lolemba, moto uabuka kukampani yopanga machesi ya Leopard Matches mumiznda umwewo.

Ndipo Lachitatu, msika wa Blantyre nawo udayaka  udayakanso Lachitatu. Zonse zili apo, ophunzira adayatsanso sukulu zaa sekondale za Thyolo ndi Lunzu zidathiridwa moto ndi ophunzira.

Nthawi zambiri galimoto zozimitsa moto zikumafika mochedwa apo ayi zikumakhala zochepa kuti zizimitse motowo.

Mneneri wa khonsolo ya Lilongwe Tamara Chafunya adati ngakhale ofesi yake ili chile kuthana ndi ngozi za moto komabe ali ndi posowekera.

Iye adati khonsoloyo ili ndi galimoto zitatu zokha zozimitsira moto—ziwiri za malita 1 200 pamene imodzi ndi ya malita 8 000.

“Apapa mutha kuona kuti tikuchepekedwa chifukwa ziwiri ndi zing’onozing’ono,” adatero Chafunya.

Chafunya adati galimotozo sizingazimitse nyumba zazitali kwambiri lomwenso ndi vuto lina. “Komanso tili ndi mavuto kuti tikatunge madzi chifukwa njira zathu zambiri anthu adamangamo. Komanso kufika malo a ngozi kukukhala kovuta chifukwa cha mamangidwe a anthu,” adatero.

Nako ku Mzuzu akuti mavuto alipo. Mneneri wa khonsolo Macdonald Gondwe adati kumeneko ali ndi galimoto zitatu zozimitsira moto koma imodzi yokha ndiyo ikugwira ntchito.

“Komanso yomwe ikugwira ntchitoyi ndi yotenga malita ochepa a madzi. Kuti malo awiri ayake moto sitingakwanitse chifukwa tili ndi galimoto imodzi yokha,” adatero iye.

Iye adatinso sangathe kuzimitsa nyumba yosanjikana katatu chifukwa cha kuchepa kwa galimotoyo.

Malinga ndi mneneri wa khonsolo ya Zomba Mercy Chaluma, mzindawo uli ndi galimoto zozimitsa moto zinayi, koma zimene zikugwira ntchito ndi ziwiri zokha.

“Uku n’kuchepekedwa ndithu,” adatero, naonjeza: “Koma ndife wokonzeka kuthandiza ngati kwina kwabuka moto.”

Mneneri wa khonsolo ya Blantyre Anthony Kasunda sadayankhe mafunso amene amati timutumizire. Ngakhale tidayesa kumuimbira iye sadayankhe foni yathu mpaka pamene timasindikiza nkhaniyi.

Koma malinga ndi mkulu wina kukhonsolo ya Blantyre, kumenekonso kuli mavuto chifukwa galimoto ziwiri zokha ndi zomwe akudalira.

Kodi nanga anthu a kumudzi akulowera kuti m’madera awo akayaka moto? Mneneri wa maboma ang’ono Muhlabase Mughogho adati m’midzimu mulibe zipangizo zozimitsira moto komabe anthu akulimbikitsidwa kuti aziyimbira khonsolo yomwe ayandikana nayo.

“Unduna wathu ukuthamangathamanga kuti pakhale yankho kwa anthuwa ngati kuli ngozi ya moto,” adatero Mughogho.

Kumayambiriro a mwezi uno, nyumba 21 m’boma la Nkhata Bay zidaotchedwa ndipo anthu anayi adaphedwa.

Anthu komanso atsogoleri awo adasowa pogwira kuti azimitse motowo ndipo ena amathira madzi pamene ena amathira mchenga.

Mfumu Masiku ya m’boma la Ntcheu yati anthu a kumudzi ndi amene ali pachiopsezo ngati kwabuka moto chifukwa alibe kolowera.

“Bola kutauniko muli ndi zida koma kumudzi kuno ndiye ndi imfa basi. Ife kuno tayandikana ndi boma la Balaka komwe ndi makilomita oposa 100 komanso kulibe zipangizo. Ndiye poti adzafike kuno angadzapeze zili bwino? Awa ndi mavuto,” idatero mfumuyo.

Related Articles

Back to top button