Chichewa

‘Lidali tsiku la Big Sunday’

Listen to this article

 

Sangwani Mwafulirwa tsopano ndi bambo, si mnyamatanso monga ena akumudziwira chifukwa dzulo pa 4 June 2016 wamulonjeza Trufena Chiwaya, mwana wa m’mudzi mwa Muleso kwa Senior Chief Somba m’boma la Blantyre kuti sadzamusiya mpaka imfa.

Sangwani ndi mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission pamene Trufena akugwira ku Western University of Malawi.

Kukwaya ya mpingo wa Living Waters ku Ndirande ndiko kudayambira kukumana kwa awiriwa. Sangwani, yemwe kwawo ndi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, akuti panthawiyo iye adalibe khumbo lothira Chichewa namwaliyu.

“Amangondisangalatsa khalidwe lake. Zachibwana ayi, zibwenzi ayi, nthawi zonse chidwi ndi Mulungu wake. Izi zidandipatsa chidwi,” adatero mneneriyu.

Sangwani ndi Trufena pano ndi thupi limodzi
Sangwani ndi Trufena pano ndi thupi limodzi

“Ndimadziwa kuti makolo anga akwiya akamva zoti ndapanga chibwenzi, komanso ndimafuna ndikafike ku University,” adaonjeza Sangwani.

Nthawi idakwana kuti awiriwa asiye kucheza zamapemphero zokhazokha. Ngakhale Sangwani adalibe maganizo, komabe Mulungu adazikonza.

Zonse zidayambika pamene mayi ake a Trufena adamwalira ku Ndirande, zomwe zidachititsa namwaliyu kuti abwerere kwawo kwa che Somba. Kuiwalana ndi Sangwani kudali komweko.

“Patatha masiku ndidayamba kumukumbukira. Kodi moyo wake uli bwanji? Kodi akulimbikirabe kupemphera? Khumbo lomuyendera lidalipo koma padalibe amene amadziwa komwe ankakhala,” adatero Sangwani.

Koma tsiku lidakwana kuti akumanenso. Uku tsopano kudali ku Big Sunday yomwe idachitikira ku Living Waters Church ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre. Kumeneko ndiye kudali kufunsana zambiri ndipo Sangwani adadziwa komwe namwaliyu akukhala.

Pakutha pa masiku angapo, Sangwani adakwawira kwa che Somba. Mofunsira njira, iye adakwanitsa kukakumana ndi namwaliyu. Apo padali pa 8 July 2001.

“Ndinenetse kuti ndinalibe maganizo ofunsira koma kukangomuona. Tikucheza, nkhani zidandithera, kenaka ndidatulutsa mawu achikondi,” adatero Sangwani.

Naye Trufena adati: “Ndinadabwa akundiuza zachibwenzi. Ndinali ndisanapangepo chibwenzi, padalibenso zoganiza koma kumuyankha pomwepo kuti zimenezo sindimapanga. Adandikakamira ndipo ine ndinayamba kudabwa naye. Kenako maganizo adandifikira kuti ngati munthuyu wayenda mtunda wautali ndiye kuti watsimikiza. Moyo wanga udavomera, ndidamulola.”

Woyera wamangitsidwa dzulo ku Fountain of Victory Church International ku Blantyre.n

Related Articles

Back to top button