Chichewa

Limbani Simenti: Kukangalika pa zoimba

Listen to this article

Ku Malawi kuno kuli oimba zauzimu ochuluka. Mmodzi mwa iwo ndi Limbani Simenti yemwe akudziwika bwino. Iyetu amadziwika kwambiri ndi nyimbo ya Ndikuoneni. CHIMWEMWE SEFASI adamupeza mnyamata wa ku Ndirandeyu ndipo adacheza naye motere:

Ndikudziwe….

Dzina langa ndine Limbani Simenti, ndimachokera chigawo cha kumwera, m’boma la Thyolo, T/A Nsabwe, m’mudzi wa Matekenya.

Adaimba ‘Ndikuoneni Baba’: Simenti
Adaimba ‘Ndikuoneni Baba’: Simenti

Kodi zoimbaimbazi mudayamba liti?

Inetu zoimbaimba ndidayamba pa kanthawi, pamene ndidali sitandade 4, koma chidwi chidayamba kundipeza pomwe ndidayamba kuimba kwaya ya Mount Sinai mu 1999. Mu 2010 pomwe ndidayamba kuimba mu Praise Team ya mpingo wa All for Jesus. Mu 2011 mpomwe ndidatulutsa chimbale changa cha Lungisani Mpiro kutanthauza kuti konzani moyo wanga.

 

Kodi nkhani zamaimbidwe umaziona bwanji pa Malawi pano?

Nkhani za maimbidwe zili bwino pa Malawi. Kungoti ubwino weniweni umaoneka munthu ukakhala ndi chidwi komanso ukaikapo mtima wako wonse, ndi kudziwa chomwe ukufuna pamoyo wako chifukwa zomwe umabzala ndi zomwe umakolola.

 

Kodi nyimbo yako ya Ndikuoneni imatiphunzitsanji?

Ndikuoneni Baba ndi nyimbo yomwe mumapezeka mphamvu. Iyi ndi nyimbo yomwe imatifupikiritsa chifupi ndi Mulungu. Mwachitsanzo, ndikamati Baba ndifuna ndikuoneni imakhala ikusonyeza ife tili paubale weniweni ndi Mulungu, ndi nyimbo yomwe ine uthenga ndimati ndikaumva ndimaona kuti Mlengi ndi amene adandipatsa uthengawo kuti ndilakhule kudzera m’nyimbo posonyeza kuti nkhawa zathu timatula kwa Yehova ndi kuonetsa ubale weniweni ndi Mulungu. Nyimbo imeneyi imapezeka m’chimbale chotchedwa Lungisani Mpiro chomwe mudali nyimbo 12 monga Uligwindi, Njoka Yokalamba, Yesu Salemphera ndi zina, pamene DVD idatuluka ndi dzina loti Ndikuoneni.

 

Kodi chaka chino Amalawi ayembekezere zotani kuchoka kwa iwe?

Ndikuwalonjeza Amalawi kuti tisanafike kumapeto a chaka chino cha 2015 ndiwapatsira chimbale chomwe chili ndi nyimbo 12, zomwe panopa ndamaliza kujambula.

Related Articles

Back to top button
Translate »