Chichewa

Lipy G: Woimba za chinyamata

Listen to this article

Masiku ano kwadza oimba achinyamata amene akumaimba nyimbo zawo zothamanga kwambiri. Kulitu anyamata monga Nepman, Blasto, Piksy ndi ena otero amene lusoli lakhazikika. Komansotu kuli anyamata ena amene akuonetsa kuti ataikapo mtima akhoza kusadabuza izi. Awa ndi monga Lipy G, amene adacheza ndi CHIMWEMWE SEFASI motere:

Ndikudziwe
Dzina langa lenileni ndi Edward Fortiner, ndine wachiwiri kubadwa m’banja la ana 6. Ndimachokera chigawo chakumwera m’boma la Nsanje.

Lipy G: Ena amatipondeleza
Lipy G: Ena amatipondeleza

Kodi kuimba zadansi udayamba liti?
Kuimba ndidayamba  pakale ndithu, nthawi imeneyo  ndili kusukulu ya sekondale, ndi pamene ndimazindikira kuti ndili ndi luso losangalatsa anthu kupyolera m’maimbidwe , munyimbo za dansi.

Kodi ndi chani chomwe unapindulako kuchoka maimbidwe?
Ine kudzera m’maimbidwe malinga ndi ndalama zomwe ndimapeza kuchoka ku zoimbaimba zandithandiza kwambiri moti pano ndinatsegula malo wojambulira nyimbo amene amatchuka ndi dzina loti Future Records. Uku ndi ku Zingwangwa mumzinda wa Blanytre.

Kupatula kuimba umachitanso chiyani pamoyo wako wa tsiku ndi tsiku?
Inetu  ndimapanga bizinesi komanso ndine katswiri pankhani yojambula nyimbo.

Kodi chimbale chako chatsopano chituluka liti? Mutu wake ndi chani?
Chimbale changa chikuyembezereka kutuka mapeto a mwezi wa October, chomwe chikhale ndi nyimbo zokwana khumi zomwe zayimbidwa mu chiyakhulo cha Chichewa ndi muchizungu. Ndipo kuyambira pa 15 October 2015 mpomwe ndiwadziwitse Amalawi zambiri.

Kodi ndi mavuto ati omwe oimba zadansinu mumakumana nawo?
Mavuto omwe timakumana nawo ndi monga kupita kuzoimbaimba koma osapatsidwa ndalama yomwe tidagwirizana, kumeneku ife timaona ngati tikuponderezedwa komanso anthu ena kuti atukule luso lathu amafuna kuti tiwapatse ndalama.

Kodi ndi anthu ati omwe unaimbako nawo nyimbo limodzi chiyambireni kuimba pa Malawi pano?
Inetu chiyambireni kuimba pa Malawi pano ndiyimbako nyimbo ndi anthu ambiri monga Blasto, Nepman. Awa ndi akadaulo komanso ndaimbako maiko akunja monga Botswana, south Africa ndi Uganda.

Pomaliza tandiuze zomwe umakonda.
Ine ndimakonda kuyimba ndi kumvera nyimbo. Nthawi zina ndimakonda kuyenda ndi kumaona malo osiyanasiyana ndi kukumana ndi anthu osiyanasiyananso.n

Related Articles

Back to top button
Translate »