Chichewa

Lule adachita chokong’ontha

Listen to this article

Lipoti la chipatala lomwe dotolo wotchuka pa zofufuzafufuza, Charles Dzamalala, watulutsa latsimikiza kuti woganiziridwa kusowetsa mwana wa chialubino, Buleya Lule adachita kuphedwa ndi shoko ya magetsi.

Izi zikutsutsana ndi zomwe apolisi adatulutsa kuti imfa ya Lule idali ya chilengedwe ndipo palibe adatasa manja ake pa iye.

Akuti achitepo kanthu: Jose

Lule adafa ali m’manja mwa apolisi. Iwo atamunjata pomuganizira kuti amakhudzidwa ndi kusowetsedwa kwa Goodson Makanjira, 14, yemwe adali mwana wachialubino wa m’boma la Dedza.

Lule amaganiziridwa kuti adadzipereka kugula thupi la mwanayo pa mtengo wa K800 000.

Mpaka pano komwe kuli Goodson sikukudziwika.

Lipoti la Dzamalala likuti thupi la Lule lidaonetsa kuti adamenyedwa, komanso kuotchedwa ndi nyetsi ya magetsi. 

Lidafotokoza lipotilo: “Ngakhale imfa ya [Lule] idadza pomuotcha ndi nyetsi ya magetsi, zikuonetseratu kuti malemuwo adachita kumenyedwa ndi zida zosiyanasiyana.”

Bungwe loyang’anira anthu a chialubino la Association of Persons with Albinism in Malawi (Apam) lati likufuna mkulu wa apolisi m’dziko muno Rodney Jose achitepo kanthu pa apolisi amene akukhudzidwa ndi imfa ya Lule.

Mtsogoleri wa Apam, Overston Kondowe, adati lipotilo langoonetseratu kuti anthu ena akukhidzidwa ndi imfa za anthu achialubino m’dziko muno. n

Related Articles

Back to top button