Nkhani

‘Luso la mpira ndilo lidandidolola’

Listen to this article

Sabata zitatu zapitazo Sindi Simtowe adamanga ukwati ndi Ardron Msowoya, mnyamata yemwe akugwira ntchito ku Inde Bank. Kwa iwo amene amadikirira pa Sindi, pepani, mtima wa njoleyi wasankha wokha.

Kodi Sindi, katswiri womwetsa zigoli m’timu ya Malawi Queens, adakumana bwanji ndi wachikondi wake? Ardron akuti lidali tsiku lomwe adasiya ntchito yake ya m’banki ulendo ku BYC kukaonera njoleyi ikudoda osati masewero.

Sindi ndi Ardron tsopano ndi thupi limodzi
Sindi ndi Ardron tsopano ndi thupi limodzi

Iye akuti wakhala akuwerenga munyuzipela za luso la Sindi kotero adaganiza zoti akadzionere yekha momwe namwaliyu amachitira.

Iye adatchera mafainolo a chikho cha OG Issa pamene timu ya Sindi, Tigresses, inkakwapulana ndi Diamonds. Ndiyetu ati udalipolipo.

Ardron atangofika pabwalopo, akuti adafunsa anthu kuti amulozere Sindi. “Atandilozera kuti Sindi ndi uyo, ndidamuitana ndi kumupatsa moni. Sindidathe nthawi chifukwa amayenera alowe m’bwalo koma akadandipatsa nthawi yaitali, ndimafuna ndipemphe nambala yake pomwepo.”

Masewero atayamba, Ardron adasangalala ndi ntchito za Sindi. Akuti amati akadumpha, kuthamanga, kuchinya zigoli, mtima wa Ardron udakanika kudzigwira ndipo adakalephera kugona.

Pakutha pa sabata zitatu adali atapeza kale nambala ya Sindi ndipo mu May 2014 macheza sadachedwe, koma apo akuti amangocheza ngati munthu ndi mnzake.

Mu August 2014 ubwenzi udayamba. “Koma kuti nditulutse Chichewa zidavuta, zimaonetsa kuti aliyense amafuna mnzake koma woyambitsa amasowa,” adatero Ardron.

“Mu June ndidamulembera uthenga wapafoni, koma sadayankhe, ndiye ndidamulemberanso wina kuti ‘darling why are you not responding?’ chiyambi cha ubwenzi wathu chidatero,” adatero mnyamatayu, amene wachita kulowola Sindi.

Ukwati udali pa 6 August ku Red Cross Church of Christ mumzinda wa Blantyre.

Sindi, womaliza m’banja la ana 11, amachokera m’mudzi mwa Mwahimba kwa Paramount Kyungu m’boma la Karonga, pamene Ardron, yemwe ndi wachinayi m’banja la ana 7, amachokera m’mudzi mwa Zolokere kwa T/A Mwankhunikira m’boma la Rumphi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »