Chichewa

Mabungwe athotha galu wakuda ku MJ

Listen to this article

 

Anthu m’boma la Mulanje omwe adakhudzidwa ndi njala kaamba ka ngozi za kusefukira kwa madzi komanso chilala kumayambiriro a chaka chino akuombera kuphazi mabungwe angapo atamva pempho lawo la kufunika kwa chakudya kuti apulumutse miyoyo yawo ku njala.

Mabungwe a Oxfam, Save the Children, Goal Malawi, Concern Universal, Irish Aid ndi ena ndiwo adachita chamuna posonkha ndalama zoposa K7 biliyoni zomwe zathandiza kuti galu wakuda yemwe adadutsa m’bomali ayambe kuona msana wa njira.

Gogo kutsekulitsa akaunthi ya Airtel Money
Gogo kutsekulitsa akaunthi ya Airtel Money

Mwambo wokhazikitsa chithandizochi udachitika ku Mulanje sabata yatha pamene akuluakulu a mabungwewa komanso mafumu adachitira umboni kuyamba kwa ntchito yothandiza anthu ovutika ndi njalawa.

Kazembe wa dziko la Norway ku Malawi, Kikkan Haugen, adati pofuna kuonetsetsa kuti palibe chinyengo pa ndondomeko yothandiza anthuwa, mgwirizano wawo wasankha kampani ya foni zam’manja ya Airtel kuti anthu azilandira chithandizo cha ndalama zogulira chimanga, mafuta ophikira ndi nyemba kapena nandolo kudzera ku kampaniyi.

Wogwirizira udindo wa mkulu wa kampani ya Airtel, Charles Kamoto, adati kampani yawo ithandizira ndondomekoyi kudzera mu Airtel Money.

“Chomwe chizichitika n’chakuti mwezi uliwonse munthu aliyense [amene ali pamndandanda wolandira nawo thandizoli] azilandira K15 800 yoti agulire thumba limodzi la chimanga, malita awiri a mafuta ophikira ndi nyemba kapena nandolo zolemera makilogalamu 10.

“Ndiye chomwe tapanga n’choti aliyense tamutsekulira akaunti ya Airtel Money yomwe azilandirirako ndalamayo. Ndipo zikalowa atha kupita kwa maejenti anthu amene ali m’boma lomwelino kukatenga ndalamazo zokagulira chakudya,” adatero Kamoto.

Malinga ndi Haugen, ndalamazi zizitumizidwa mwezi uliwonse kuti anthu asatuwe ndi njala.

“Takhutira kuti ndalamazi zithandiza anthu enieni ovutikitsitsa,” adatero Haugen. n

Related Articles

Back to top button