Nkhani

Mademo ayambika

Gulu lomwe lakhala likudzudzula boma la Tonse Alliance chilowereni m’bomamo la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) mogwirizana ndi mavenda a bizinezi zing’onozing’ono akonza zionetsero zomwe zikhudze dziko lonse.

Maguluwa ati akonza zionetserozi zomwe ziyambire mumzinda wa Lilongwe pa 16 December 2020 chifukwa chokwiya ndi kusamva komanso kusalabadira za mavuto a anthu komwe Tonse Alliance yaonetsa chitengereni boma.

Pazionetsero za HRDC, chimbaula cha polisi chidaotchedwa

Malingana ndi kalata yomwe Cdedi idatulutsa Lachitatu, boma silidayankhebe kalikonse pa nkhawa ndi mavuto omwe bungwelo komanso mavenda adalipatsa pa 23 November 2020 kuti liyankhe pasadathe masiku 14.

“Masiku 14 omwe Cdedi limodzi ndi mavenda a bizinesi zing’onozing’ono m’mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe adapereka kuti boma liyankhe pa nkhawa ndi mavuto awo atha koma palibe chomwe chachitikapo.

“Izi zatipatsa chithunzithunzi choti bomali ndi lomva zake zokha osati za anthu ngati momwe ankatilonjezera pa kampeni kotero takonza zionetsero za dziko lonse kuyambira ndi mzinda wa Lilongwe Lachitatu pa 16 December 2020,” yatero kalatayo.

M’miyezi yomalizira yaulamuliro wa Democratic Progressive Party (DPP) yomwe idalandidwa boma ndi Tonse Alliance pachisankho chobwereza pa 23 June 2020, dziko la Malawi lidayakadi moto wamalawi ndi zionetsero zomwe linkatsogolera gulu lomenyera ufulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC).

Cholinga cha zionetserozo chidali kukwiya kwa Amalawi ndi mchitidwe omwe bomalo linkapanga osamvera za anthu, kukula kwa katangale, kusatsata malamulo, nkhanza komanso ulamuliro wosalabadira za mavuto a anthu.

M’kalata yake, Cdedi yati zambiri mwa izi zikuoneka m’boma la Tonse Alliance n’chifukwa chake lakonza zionetserozo kuti mwina nkhawa ndi madandaulo ake angamveke kutali n’kuyankhidwa.

Nkhawa zambiri zomwe bungwelo ndi mavenda akudandaula ndi kuchuluka kwa nzika za maiko ena zomwe zikuphangira mabizinesi ang’onoang’ono oyenera nzika za Malawi, njengunje wa mupologalamu ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo ya Affordable Inputs Programme (AIP), kukondera pomanga anthu akatangale ndi amirandu ina zomwe zikuyipira anthu a ku mmwera.

Nkhawa zina ndi monga kuthotha akabaza wa njinga zamoto osakambirana nawo kukweza malipilo a aphungu ndi K100 pa K100 iliyonse pomwe ogwira ntchito m’boma ena adawakwenzera mdi K10 pa K100 basi.

Kalatayo yapitirira kunena za kusalabadira kwa boma pa mfuu wa anthu a ku Mulanje ndi Thyolo omwe malo awo adalandidwa ndi azungu ndipo eni ake n’kumakhala ngati akapolo komanso kuyiwaliratu mfundo zake zonse za pa kampeni.

Kadaulo wa ndale George Phiri wati vuto lomwe lilipo ndilakuti boma la Tonse silidaonetsebe luntha lokwaniritsa malonjezo ake pa kampeni yake chifukwa Amalawiwo adalipatsa voti kaamba ka malomjezowo.

Iye adati nkhani ya nthawi yomwe bomali lakhala pampando siyogwira chifukwa nkhani yaikulu ikadaoneka m’bajeti momwe zambiri zomwe Amalawi adalonjezedwa mulibemo ndiye Amalawi ayenera kukhala ndi mkwiyo.

“Zambiri zikupotoka kanthawi komweka ndiye anthu akamawona zimenezi mukanthawi komweka mitima yawo yayamba kale kuthawa kuti ziwathandiza. Ntchito 1 miliyoni zili kuti, apa aphungu ndi awa akweza ndalama mosalabadira,” watero Phiri.

Nduna ya zofalitsa nkhani Gospel Kazako yemwenso ndi mneneri wa boma wati nkhaniyi yangoona kulowera kumeneku chifukwa sizoona kuyembekezera kuti boma lingathane ndi mavuto omwe adapelekedwawo m’masiku 14 okha.

Related Articles

Back to top button