Nkhani

Mafumu aluzanitse mtundu

Listen to this article

Nthawi ya mwambo wa Achewa wa Kulamba yafikanso. Paja chikhalidwe ndiye mizu ya mtundu ulionse.

Achewa amasonkhana malo amodzi monga mwa mwambo wawo, kupereka zoonga kwa mfumu yawo komanso kukambirana momwe anthu awo akukhalira m’madera awo.

Tikumbuka bwino lomwe chaka chatha kumwambowu, mafumu a Chichewa adadandaula momwe ntchito ya makuponi imayendera.

Pambali pa kukamba za momwe anthu akukhalira, nthawiyi imakhalanso yoyanjanitsa Achewa a ku Zambia, Malawi ndi Mozambique. Kumva anthuwa akulankhula chilankhulo chawo, umazindikira kuti malire amene adaika atsamunda sadafike poiwalitsa anthuwo kuti ndi amodzi.

Ife nthawi iyi timayiremekezanso pajatu aliyense ali ndi ufulu wochita zimene chikhalidwe chake chimamulamula kuti achite mosaphinja ufulu wa munthu.

Nthawiyi tikufuna Amalawi tikhale limodzi. Tigwirizane ndipo timvetsetsane, ngati pena zalakwika tikambirane. Ichi tikukhulupirira kuti ndicho chingamange Malawi wabwino.

Lathu ndi pempho kwa mafumu aakulu a Achewa muno m’Malawi Paramount Chief Lundu komanso Senior Chief Kaomba kuti akadabwera poyera ndikuuza mtundu wa Amalawi ngati akupita kumwambowo kapena ayi.

Mafumu sayenera kukhala oyamba kugawanitsa mitundu chifukwa izi zimadza ndi zovuta zambiri.

Related Articles

Back to top button
Translate »