Nkhani

Mafumu ‘okwatitsa’ ana athothedwa

Listen to this article
  • Kachindamoto achotsa mafumu anayi
  • Ana 549 abwerera kusukulu ku Dedza

Kampeni yothamangitsa ana kubanja kuti abwerere kusukulu yafika pagwiritse m’boma la Dedza pamene T/A Kachindamoto wathotha mafumu anayi pokolezera maukwatiwa.

Kachindamoto: Tidagwirizana malamulowa
Kachindamoto: Tidagwirizana malamulowa

Ngakhale gawo 11 (1) la malamulo okhudza mafumu la m’chaka cha 2000 limati pulezidenti wa dziko yekha ndiye ali ndi mphamvu yochotsa mfumu, Kachindamoto wati palibe cholakwika iye kuthotha mafumuwo.

Iye wati mphamvuzo akuzitenga m’malamulo amene m’dera lake adakhazikitsa chaka chatha wolanga mfumu yovomereza maukwati wa ana. “Tidakhazikitsa malamulo athu amene tidavomerezana ndi anthu komanso mafumu tonse kuno kuti ngati papezeka mfumu yopsepserezera ukwati wa ana, imeneyo iyenera kuchotsedwa.

“Ichi nchifukwa chake mafumuwa atapezeka olakwa, ndidawaitana anthu onse ali pamenepo pamene ndidalengeza kuti ufumu wawo watha. Iwo achotsedwa chifukwa choswa malamulo,” adatero Kachindamoto.

Koma mneneri wa maboma ang’ono Muhlabase Mughogho wati ngakhale pulezidenti ndiye ali ndi mphamvu yochotsa mfumu, malamulo amene Kachindamoto ndi anthu ake adakhazikitsa alinso ndi mphamvu yothotha mfumu ngati yalakwitsa.

“Nkhani imeneyo ife sikutikhudza, imeneyi ndi yawo. Ngati adagwirizana kuti mfumu izichotsedwa ikasemphana ndi malamulo amene adagwirizana, ndiye palibe nkhani pamenepa, amenewo ayenera kumvera zomwe adagwirizana,” adatero Mughogho.

Kachindamoto akuti kupatula anthu ndi mafumu am’dera lake amene adagwirizana ndi malamulowa, nawo amabungwe omenyera kuti ana apite kusukulu akusangalala ndi ndondomekoyi.

Iye wati, adasankha kuti mfumu izilandira chilango chifukwa ukwati kapena chinkhoswe si zimachitika m’dera popanda mfumu kudziwa.

“Kukakhala ukwati kapena chinamwali, banja lomwe likupangitsalo, limakadziwitsa mfumu pamene amakapereka nkhuku. Apa ndiye kuti anthuwa ali ndi chilolezo chochititsa ukwatiwo.

“Podziwa izi, nchifukwa tidati mfumu yomwe ilandire nkhukuyo kapena yomwe ivomereze ukwatiwo idzalangidwa poichotsa pampando,” adatero Kachindamoto.

Chifukwa cha malamulowa, Kachindamoto wati ana 549, amuna ndi akazi omwe abwerera kusukulu pamene asiira ana awo kwa makolo.

Iye adati mafumu amene achotsedwawa akhala akuvomereza ukwati wa ana polandira nkhuku kwa eti ukwati zomwe ndi zosemphana ndi malamulo awo.

“Mafumuwa akhala akulandira nkhuku ngakhale amadziwa kuti amene akuchititsa ukwatiyo ndi mwana woyenera apite kusukulu. Mafumu atatu ndidawachotsa chaka chatha pamene inayo ndidaichotsa chaka chomwe chino,” adatero Kachindamoto yemwe ali ndi magulupu 51.

Nyakwawa Galuanenenji yomwe ufumu wake udatha povomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15, yati idadandaula kuti ufumu wake watha komabe sadaone cholakwika.

“Malamulo tidavomereza tokha, komabe pena zidavuta pamene ndidavomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15. Adandiitana pagulu ndipo gogochalo adalengeza kuti ufumu wanga watha. Mutu udakula, ndipo m’mimba mudatentha kuti ufumu wanga watha,” adatero Galuanenenji.

“Panopa ndidakapepesa kwa gogochalo ndipo ndidakathetsanso banjalo, panopa mwanayo wabwerera kusukulu. Chifukwa choti ndidapepesa komanso kuti ukwatiwo ndidakathetsa, amfumuwa andibwezeretsa pampando,” idatero nyakwawayi.

Mmodzi mwa atsikana amene abwerera kusukulu, Judith Kabango wati ndiwokondwa ndi malamulo amene mudzi wawo udagwirizana.

“Ndidatengana ndi mwana mnzanga wapasukulu. Panthawiyo n’kuti ndili sitandede 7, pano ndili 8 ndipo mayeso apitawa ndidakhala nambala 4. Ndikufuna ndiphunzire ndipo ndikufunitsitsa ndidzagwire ntchito ya utolankhani,” adatero mtsikanayu yemwe mwana wake ali ndi zaka 4.

Bambo ake a Judith, Stanstance Kabango am’mudzi mwa Kalonga ati ndiwokondwa kuti mwana wawo tsopano wabwerera kusukulu.

Iwo ati adali wokhumudwa kuti mwana wawo yemwe adamukhulupirira kuti adzapita patali ndi sukulu wakalowa banja.

Related Articles

Back to top button