Nkhani

‘Mafumu sanunkha kanthu pandale’

Listen to this article

Kafukufuku amene achita akadaulo a zandale m’dziko muno wasonyeza kuti ngakhale mafumu ena amayesetsa kusanthula momwe Amalawi akuganizira pandale, Amalawi salabadira zonena za mafumuzo.

Mmodzi mwa akatswiriwo, Happy Kayuni amene amaphunzitsa ukadaulo pandale ku Chancellor College, adati zotsatira zimene adapeza adzazikhazikitsa pa 17 March ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre.

Mafumu sayenera kuika mlomo pankhani za ndale

Izi zikudza patangotha sabata kuchokera pamene anthu ena adakuwiza Paramount Lundu pamaliro a mfumu Kabudula ku Lilongwe pomwe mwa zina adati chipani cha MCP chidalamulira dziko lino zaka 31 ndipo sichidzalamulilanso kuchokera mu 1994 pomwe chidachoka m’boma. Lundu adatinso chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndicho chidzalamulire mu 2019.

Koma polankhula ndi Tamvani, Kayuni adati kafukufukuyo adapeza kuti mafumu amalemekezedwa ndi kukhulupiliridwa pankhani za miyambo yawo osati popanga ganizo la ndale.

“Tikatulutsa zotsatirazo, anthu adzadzionera okha kuti anthu amalemekeza ndi kukhulupilira mafumu pankhani za chikhalidwe chawo koma alibe chikoka pakapangidwe ka ganizo la munthu amene asankhe pa ndale,” adatero Kayuni.

Kayuni adakana kutambasula bwino kuti kafukufukuyu adamuchita nthawi yaitali bwanji, ndi anthu angati, njira yomwe adatsata pofunsa mafunso komanso mafunso amene amafunsidwa. Iye adati zonse adzazitambasula bwino akamukhazikitsa.

Iye wati chanzeru chomwe mafumu angachite nkuphathirira ku udindo wawo ndi kumalimbikira ntchito yawo mmalo motaya nthawi ndi zandale powopa kutsukuluza ulemu omwe ali nawo.

Pa zomwe mafumu ena akhala akunena kuti amayenera kukhala mbali yaboma, Kayuni wati ichi n’chilungamo chokhachokha koma waunikira kuti mpofunika kutanthauzira bomalo molondola.

“Mpofunika kutanthauzira bwinobwino liwu lakuti boma chifukwa mwina mafumu oterowo amaona ngati boma n’chipani cholamula pomwe si choncho. Boma limagawidwa patatu: Mtsogoleri ndi nduna zake, aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mabwalo oyendetsa.

“Akamati amakhala mbali ya boma, sakulakwa koma aziganizira tanthauzoli kuti iwo ngopanda mbali ndipo ntchito yawo n’kutsogolera anthu awo pankhani zamakhalidwe ndi chitukuko. Ndale n’za anthu ena,” adatero Kayuni.

Polankhula ku maliro a T/A Kabudula, Senior Chief Lundu adaweruziratu kuti chipani cha DPP ndicho chidzapambane pachisankho cha 2019 ndipo kuti kaya wina afune kaya asafune, mafumu ena m’dziko muno sadzaleka kusapota mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi chipani cha DPP.

“Ngati tili pansi pa ulamuliro wa Mutharika ndi chipani cha DPP, chotiletsa kumusapota nchiyani? Choti mudziwe nchakuti chipani cha DPP chikuyenera kulamula mpaka 2019 ndipo chidzapitiliza kuchoka apo,” adatero Lundu kumaliroko.

Iye adapitiriza kunena kuti chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chomwe mtsogoleri wake Lazarus Chakwera adali pa maliro pomwepo chisamalote zodzalamuliranso ndipo kuti kwake kudatha momwe chidatuluka m’boma ngati chipani cholamula.

Chakwera atafunsidwa ndemanga yake ndi Tamvani pa nkhaniyi adati alibe mau aliwonse kenako nkuseka.

Oyendetsa nkhani za mafumu ku unduna wa Maboma ang’onoang’ono Lawrence Makonokaya adati timutumizire mafunso omwe tikuyembekezera mayankho ake.

Zotsalira

Tikuchezanso ndi kadaulo wina amene adacchita nawonso kafukufukuyo.

Related Articles

Back to top button
Translate »