Nkhani

Magulu othandiza odwala edzi akufa

Listen to this article

Chitsime chidauma! Moti magulu 132 mwa 150 olimbana ndi mlili wa edzi mu mzinda wa Mzuzu afa pamene ena 18 ali mwakayakaya.

Mavutowa adayamba m’chaka cha 2017 pamene bungwe la Global Fund lidaleka kupereka ndalama ku bungwe la National Aids Commision (NAC) kaamba koti silimagwiritsa ntchito moyenera ndalamazo.

Global Fund yakhala ikupereka ndalama zogwirira ntchito zolimbana ndi edzi ku mabungwe a ActionAid ndi World Vision.

Mmbuyomu NAC ikalandira ndalamazo imapereka zina ku magulu olimbana ndi edzi a m’midzi. Padakali pano, zinthu zidasintha.

Wapampando wa magulu a mu mzinda wa Mzuzu, a Solister Kasambara, adati kwa zaka zisanu tsopano sakulandira ndalama.

“Mzinda wa Mzuzu udali ndi magulu 150 ndipo 132 adafa n’kutsala 18. Izi zachititsa kuti ntchito yothandiza odwala edzi m’midzi ikule moti tikulephera kufikira aliyense,” adatero a Kasambara omwe ndi mkulu wa gulu la Lujeso Community Based Organisation (CBO).

A Michael Kameta, a gulu lina lothandiza odwala edzi m’boma la Nkhata Bay, akugwirizana ndi a Kasambara.

A Kameta, wochokera ku Mtisunge Aids and Community Development Support Organisation (Macodeso), adati bungwe la ActionAid lomwe lakhala likulandira ndalamazo, silipereka zina ku maguluwo.

Iwo adati mwa magulu 104 omwe amagwira ntchito zothandiza odwala edzi m’bomalo, 46 adafa, 58 ndiwo atsala.

Mkulu wa ActionAid, a Assani Golowa, adati akhala akulandira ndalama kuchokera ku Global Fund mpaka December wa chaka chatha.

Iwo adati padakali pano World Vision ndiyo ikulandira ndalamazo.

“N’zoona njira yomwe ActionAid imagwiritsa ntchito idali yosiyana ndi yomwe NAC imatsatira ikalandira ndalama kuchokera ku Global Fund.

“NAC ikalandira ndalama imazipereka ku magulu olimbana ndi edzi a m’midzi, koma ife timazipereka kwa mabungwe omwe amagwira ntchito ndi mabungwe ena,” adatero a Golowa.

Iwo adatsimikiza kuti n’zoona magulu adafa potsatira kusinthaku.

“Chomwe mwina sitidachite bwino n’kufotokozera maguluwa kuti ndondomeko ya ndalama za Global Fund yasintha.

“Anthu ayenera kudziwa kuti  njira zonse zomwe boma kapena mabungwe amatsatira zimafikira anthu a m’midzi,” adatero a Golowa.

Mkulu wa Malawi Health Equity Network (Mhen), a George Jobe, adati pafunika kafukufuku kuti anthu adziwe momwe kusinthaku kuchepetsera kufala kwa HIV m’dziko muno.

Global Fund idasiya kupereka ndalama ku NAC chifukwa zimalowa m’matumba mwa anthu osolola moti NAC idauzidwa kubweza ndalama zomwe silidagwiritse bwino ntchito.

Related Articles

Back to top button