Nkhani

Makhansala aderera alawansi

Listen to this article

Kucha kwa Lolemba lapitali Amalawi adadzuka ndi nkhani yododometsa kuona adindo (makhansala) akulalata poyera kudelera alawansi ya K20 000 ndipo akunena modzithemba kuti iwo amayembekezera kuti alawansiyo ikhala K200 000 khansala aliyense.

Koma mongokumbutsira, K20 000 yomwe makhansalawo amadelera ndi yokwanira kugula matumba anayi afetereza otsika mtengo yemwe alimi ambiri kumudzi akusowa ndi chenje chokwanira K2 000 pamwamba pake.

Chakwera adakumananso ndi makhansala a ku Mzuzu koma izi sizidaphulike

Kanema ya makhansala a mumzinda wa Blantyre yomwe Tamvani ikusunga mpaka lero ikuwonetsa makhansalawo akulalata kuti zomwe akuwona (polandira K20 000 ngati alawansi) sizikugwirizana ndi Kanani yemwe amayembekezera.

“Kodi Kenaniyo ndi ameneyu? Kumalandira K20 000 pomwe kale anzathu akakumana ndi Pulezidenti ankalandira K200 000. Ayi sizoona ndiye bolanso kalelo,” akutero makhansala mukanemayo.

Lamulungu lapitalo, makhansala a mumzinda wa Blantyre adakakumana ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera kunyumba ya boma ya Sanjika ndipo utatha mkumano wawo adapatsidwa K20 000 aliyense ngati alawansi yokhalira pamkumanowo.

Koma mkulu woyendetsa mapologalamu kubungwe lowona zoti zinthu zikuyenda m’chilungamo ndi mtendere la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) Boniface Chibwana wati izi zikuonetseratu poyera kuti adindo m’dziko muno sazindikira chomwe adakhalira pampando.

“Zikungoonetsa kuti tikadali ndi maganizidwe a kalekale woti pampando mpodyera kuiwala kuti kukhala pampando ndi mpata wotsogolera anthu. China chomwe adindowa akuiwala n’choti chomwe ana akuona lero chikukhazikika mwa iwo choncho adzapanga zomwezo nthawi yawo yokhala pampando ikadzafika,” adatero Chibwana.

Iye adati potengera zomwe zili mkanemayo, zikuwonetseratu kuti makhansalawo adalibe ntchito ndi zokambirana zomwe adali nazo ndi Pulezidenti koma kuti mitima yawo idali pa ndalama basi.

“Mpata okumana ndi Pulezidenti ndi wosowa kwambiri moti makhansalawo akadakhala ena akadagwiritsa ntchito mpatawo kukambirana ndi Pulezidenti nkhani zachitukuko m’madera mwawo,” adatero Chibwana.

Koma mkulu oyendetsa ntchito za likulu la makhansala la Malawi Local Government Association (MALGA) Charles Chunga wati anthu akutengera zomwe zili mukanemayo pamgong’o.

Iye adati makhansalawo amangoseleula pa zomwe amachita ndi kunenazo koma osati kuti adali ndi mtima woderera alawansiyo.

“Palibe lamulo kapena ndondomeko yomwe imanena kuti alawansi ya makhansala ndizingati. Iwo amakumana ndikukambirana ndi aliyense yemwe wawafuna ndipo zimatengera owayitanayo kuti awapatsa alawansi yochuluka bwanji ndiye sikuti aphunguwo amadelera,” watero Chunga.

Iye adati likululo lilibe ndondomeko yeniyeni yokhazikitsira mwambo pakati pa makhansala ndipo limagwiritsa ntchito makhansala omwewo kudzudzula ndi kuwongola anzawo omwe awonetsa khalidwe losokonekera koma pakali pano palibe khansala yemwe wafika pofunika mwambo.

“Anthu akukokomeza kwambiri nkhaniyi chifukwa munthu olalata saonetsa nkhope yoseka ngati momwe makhansala aja akuwonekera mukanemayo,” adatero Chunga.

Woyang’anira zofalitsa nkhani kunyumba za boma Sean Kampondeni adauza atolankhani Lolemba kuti boma la Tonse Alliance silidabwere kudzadzadza matumba a anthu ndi ndalama.

“Boma ili lidabwera kudzakonza zinthu ndi kubweretsa chitukuko osati kudzagawa ndalama ayi ndiye sitingasinthe chikonzero chathu chokonza dziko kuti tiyambe kugawa ndalama nkumawoneka abwino,” adatero Kampondeni.

Ndipo Chibwana adati njira yokhayo yothana ndi nthenda yongofuna kulandira n’kukhazikitsa lamulo loona za zipani za ndale momwe mfundo ina ndi kuonetsetsa momwe zipani zimapezera ndi kugwiritsira ntchito ndalama.

Anthu osiyanasiyana pamchezo wa pa Intaneti apereka ndemanga zodzudzula zomwe makhansalawo adachita.

Related Articles

Back to top button
Translate »