Chichewa

Makuponi adza ndi misonzi

Listen to this article

 

 

Bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) komanso alimi ena apempha boma kuti likonzenso ndondomeko ya feteleza wotsika mtengo.

Pempholi ladza pamene zadziwika kuti kampani zimene zidapatsidwa mwayi wogulitsa alimi feteleza zikulephera kufikira madera onse komanso kuti mitengo yawo ndi yoboola m’thumba.

Clara Nyandula wa ku Bamba kwa T/A Phambala m’boma la Ntcheu wakhala akugulira feteleza wake pasukulu ya Matchereza chiyambireni ndondomeko yotsika mtengoyi.  Pasukulupa akuti pamafika feteleza wa midzi 20 ya mwa T/A Phambala. Chaka chino akuti feteleza sadafike.

Banda kutha mtunda atagula feteleza

“Chimanga chafika popota, koma feteleza sitinagule. Pachifukwachi, tidaganiza zopita m’boma la Balaka komwe tidakagula. Tidauzidwa kuti thumba ndi K7 000 la makuponi koma kukafika uko tagula thumba pa mtengo wa K12 000,” adatero Nyandula.

Kuchoka m’boma la Balaka kupita ku Ntcheu, thumba limodzi akuti amalipira K1 300. Zonse akuti zimalowa K14 000 kuti thumba likafika m’madera awo.

“Zandiwawa kwambiri, sindidayembekezere kuti zifika pamenepa, ndi bwino ndondomeko ingotha chifukwa sindidaone ubwino wake,” adatero mlimiyu.

Naye Frank Banda wa m’mudzi mwa Namkumba kwa Senior Chief Somba m’boma la Blantyre akuti nthawi zonse amagula feteleza pa Mpemba koma chaka chino feteleza sadafike.

Banda, amene tidamupeza m’chikhamu cha ofuna kugula feteleza kukampani yogulitsa feteleza ya Optichem mumzinda wa Blantyre, adati ndondomeko ya chaka chino ndi yozunza alimi.

“Ndinabwera kuno kuti ndidzagule matumba awiri omwe ndi K14 000, koma kudabwa akundiuza kuti thumba limodzi ndi K8 500,” adatero iye.

Nako ku Zomba zasokonekera. Khansala wa wodi ya Mtungulutsi ku Zomba Lisanjala, Wilson Likusa, wati wodi yake muli anthu 2 000 amene adalandira makuponi koma matumba 200 okha ndiwo adafika.

“N’zachisoni, chifukwa ngakhale mtengo wa thumba la feteleza ndi K11 000 komanso kuti ugule ukuyenera udutsire mwa munthu wina,” adatero iye.

Senior Chief Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay yati mavuto a chaka chino aposa a zaka zonse ndipo ngati boma silisamala zinthu zipitirira kuipa.

“Tingolakwapo apa, tatopa ndi kudikira feteleza. Sitikudziwa kuti titani chifukwa madandaulo athu sakumveka. Alimi sadagule feteleza mpaka lero pamene chimanga chikupota, ndi zoona izi?” adafunsa Kabunduli.

Izi zakhumudwitsa mkulu wa bungwe la Farmers’ Union of Malawi, Alfred Kapichira Banda yemwe wati alimi sangapeze phindu ngati boma silichotsa zotsamwitsazi.

Iye adati: “Alimi ambiri sadagule feteleza. Ku Dowa, Kasungu mpaka Salima alimi akudandaula nkhani yake yomweyi. Komanso ku Dowa alimi ena akugula feteleza pa K24 000 thumba limodzi.

“Uku ndi kupha alimi, palibe tsogolo ndipo tikupempha boma kuti lithamange kumva mavuto amene alimi akukumananawo ndipo akonze zinthu zisadavutitsitse,” adatero Banda.

Mneneri wa unduna wa zamalimidwe, Hamilton Chimala, wati ndondomekoyi yabwera moyeserera kaye ndipo zomwe akufuna ndi kuthana ndi chinyengo.

“Tidagwirizana kuti kampanizo zikwanitsa kufikira alimi, ndiye ngati n’zoona  kuti alimi ena mpaka lero sadagule feteleza chifukwa akumusowa, ndiye ndi zachisoni,” adatero Chimala pamene adati unduna wawo uwunguza zotsamwitsa zonse.

Boma lidasintha ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengozi pamene lidaika K15 000 pathumba lililonse lomwe mlimi agule ndi koponi.

“Thumba lililonse, boma lidaikapo K15 000. Kusonyeza kuti mlimi azigula thumbalo motsika mtengo ndi kuponi ndipo ifeyo tidzapatsidwa kuponiyo ndikulipira kampani yomwe mlimiyo adakagula feteleza wake.

“Izi zikusonyeza kuti mitengo izikhala yosiyana, zili kwa mlimi kusankha komwe akufuna kukagulira feteleza wake,” adaonjeza.

Izi zikusonyeza kuti ngati kampani ikugulitsa feteleza pamtengo wa K23 000 ndiye kuti mlimi azipereka K8 000 basi. Izi zikusiyana ndi chaka chatha pamene alimi amagula thumba pa mtengo wa K3 500 kulikonse. n

Related Articles

Back to top button