Nkhani

Malawi ali mu mdima

Zasokonekera! Malawi ali pamoto wosaneneka ndi kuzimazima kwa magetsi. Anthu akumudzi akugona kuchigayo kudikira magetsi pamene alimi a ng’ombe zamkaka akutaya mkaka.

Ndi Loweruka usiku cha m’ma 10 koloko pamene timafika pachigayo cha Muhiriri m’dera la mfumu Kasisi m’boma la Chikwawa.

Si zidaonekenso: Amayi kugona m’chigayo podikira kugayisa chimanga

Anthu 16, atatu mwa iwo abambo, ali pachigayopa kudikira magetsi. Anayi okha ndiwo ali maso pamene onse agona.

Matumba a chimanga komanso mapira andandana kuti magetsi akayaka agayise. Magetsiwatu akuti adazima Lachisanu mmawa.

Pafupi nane pali mayi wachikulire, ndi wothodwa. “Sindikudziwa kuti ayaka nthawi yanji, koma ndabwera pano mmawa cha m’ma 7,” adatero mayiyu, Ezelesi Stanton wa zaka 60.

Ngakhale atayaka, Stanton sangabwerere kumudzi chifukwa wayenda mtunda wa makilomita 8.

Awa ndiye ndi mavuto adzaoneni: Anthu akudikira magetsi ayake pa chigayo cha ku Chikwawa

“Kunyumba kulibe ufa, ndasiya ana ndi bambo. Kuti ndibwerere ndiye sitikadya chifukwa ufa udatheratu,” adatero mayiyu.

Awa ndiwo mavuto amene akungana kumudzi pamene bungwe lopanga magetsi la Electricity Generation Company of Malawi (Egenco) likungopanga pafupifupi theka la magetsi amene dziko lino likufuna.

Izi zikupangitsa kuti anthu ena, monga aku Chikwawa, azitha masiku awiri osaona magetsi.

Eleni Kalavina wa m’mudzi mwa Chikalumpha akuti mwezi wa November wokha wagona kuchigayo kanayi, kudikira magetsi kuti agayise.

Pamene timafike pa chigayopa, Kalavina adali m’tulo. Iye adadzidzimuka pemene mwana wake wa miyezi 7 amalira. Iye adadzuka ndi kumuyamitsa.

Pachigayopatu pali ana oyamwa anayi amene agona kumimba kwa amayi awo.

“Ambuye adzatitenge, dziko lino latopetsano,” Kalavina adatero. “Mwina n’kukaona zina kumwambako.”

“Kodi Ambuye abwera liti? Tatopa abale.” Iye adati kuzimazima kwa magetsi kukuzuza moyo wawo komanso mabanja awo.

“Nthawi zina amunanga amandikaniza kuti ndisadzagone kuno poganizira kuti mwina ndikukayenda ndi amuna ena pamene si choncho,” adatero.

Pamene nthawi imathamangira 12 koloko usiku, bambo wina adafika pamalopo mokuwa. “Kodi kuli akazanga kumeneko?”

Bamboyu, Davie Kachiza wa zaka 49, amachokera m’mudzi mwa Josamu m’dera la mfumu Katunga-mtunda wa makilomita 7-kudzasaka mkazi wake.

“Ndakhala ndikumudikira koma mpaka pano sakubwera. Ndanyamuka cha m’ma 9 koloko usiku kuti ndisake chigayo chomwe ali,” adatero mkuluyu.

Kunyumba wasiya mwana wa zaka 14 ndi wina wa zaka 9. Koma pachigayopo padalibe mkazi wake ndipo adatsetserekera ku chigayo china komwe adakamupeza.

Kachiza adapempha atsogoleri kuti athetse mavuto amene akunga Malawi. “Tivomereze zinthu sizili bwino m’dziko muno. Malawi waipa,” adatero Kachiza.

Nyakwawa Zakaliya idati anthuwa alibe kothawira chifukwa amayenera ayende mtunda wa makilomita 17 kuti akapeze chigayo cha dizilo.

Iye adati ali ndi mantha ndi anthu ake. “Kugona kuchigayo komanso kumayenda ndi usiku kusaka magetsi, ndi zachisoni, anthuwa atha kuchitidwa chipongwe komanso kunyumba kwawo akumasiya ana pamene makolo ali kuchigayo,” adatero Zakaliya.

Pamene timachoka pa chigayopo m’mama wa Lamulungu n’kuti magetsi asadayakebe ndipo akuti adayaka cha m’ma 5 madzulo a Lamulungu.

Mavutowa sadasiye malo, ku Ntcheu, Thyolo ndi Nkhata Bay, anthu akuti ayamba kumasinja pamanja pamene ena akuyenda mitunda yotalika kusaka chigayo cha dizilo.

“Tayamba kusinja pamanja kuno,” adatero mfumu Kabunduli ya m’boma la Nkhata Bay.

“Boma lisagawe pakati Escom. Izi ndi zomwe zikubweretsa mavutowa. Aleke Escom izipanga ndi kugulitsa yokha magetsi,” idaonjeza choncho mfumuyo.

Samuel Mugwa, mlimi wa ng’ombe za mkaka wa kwa Goliati m’boma la Thyolo, akuti akusowa kogulitsa mkaka chifukwa makampani ogula mkaka ayimika kaye chifukwa cha kuzimazima kwa magetsi.

“Poyamba ndimapanga K75 000 pa mwezi, patsiku ndimagulitsa malita 18. Pano bizinesi yasokonekera chifukwa asiya kutigula. Mkaka ukuwonongeka chifukwa cha magetsi,” adatero mkuluyu.  n

 

Related Articles

Back to top button