Nkhani

Malawi ikuswapangano la UN

Listen to this article

Malawi ikuswa pangano la zaumoyo la bungwe la United Nations (UN) lomwe idasaina ku Abuja m’dziko la Nigeria.

Akatswiriwa akuti izi zichititsa kuti mavuto azaumoyo omwe ali m’dziko muno azingopitirira.

Muli mavuto adzaoneni m’zipatala za boma

Kudzera mu mgwirizana wa Abuja, atsogoleri a maiko adalonjeza kuti azipereka K15 pa K100 iliyonse yomwe ili mu bajeti ku ntchito zaumoyo.

Cholinga cha mgwirizanowo chidali kuchepetsa mavuto omwe maiko, kuphatikizira la Malawi, akukumana nawo pa nkhani ya zaumoyo.

Mwachitsanzo, ena mwa mavuto omwe dziko la Malawi likukumana nawo ndi kusowa kwa mankhwala, zipangizo ndi kuchepa kwa ogwira ntchito m’zipatala zaboma.

Ngakhale Malawi idasainira mgwirizanowo, kafukufuku akuonetsa kuti likulephera kupereka K15 pa K100 iliyonse yomwe ili mu bajeti ku ntchito zaumoyo.

M’zaka zammbuyomu Malawi imapereka pafufupi K10 pa K100 iliyonse yomwe inali mu bajeti, koma chaka chino ndalamayi yatsika kufika pa K6.

Mwachitsanzo, m’chaka cha 2017/18 bajeti ya Malawi idali pa K1.3 thililiyoni ndipo unduna wa zaumoyo udalandira K129 biliyoni zomwe zikuimira K9.9 pa K100 iliyonse ya mu bajetiyo.

M’chaka cha 2018/19 bajeti idali pa K1.5 thililiyoni ndipo unduna udapatsidwa K86.7 biliyoni zomwe zikutanthauza kuti udalandira K9.8 pa K100 iliyonse ya mu bajetiyo.

Bajeti ya chaka chino (2019/20) ndi K1.7 thililiyoni ndipo unduna wa zaumoyo wapatsidwa K87 biliyoni yomwe ikuimirira K5.9 pa K100 iliyonse yomwe ili mu bajetiyi.

Mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adati kuchepa kwa ndalama kutha kuika dziko lino pa mavuto a akulu azaumoyo.

“Maika akafika popangana mpaka kusainirana amakhala atavomera mfundo ndi ndondomeko zonse za mgwirizano wawo, komanso amaunika kuti atha kuzikwaniritsa,” adatero Jobe.

Nayo komiti ya zaumoyo ya ku Nyumba ya Malamulo yati ndi yokhudzidwa kuti dziko lino likulephera kukwaniritsa panganolo.

“Dziko la Malawi likuyenera kupeza njira zokwaniritsira pangano la Abuja. Ili si pempho, koma mgwirizano,” adatero Deus Gumba powerenga lipoti la komiti yake m’Nyumba ya Malamulo.

Mhem ndi komitiyo apempha boma kuti lionjezere ndalama zomwe lapereka ku undunawo.

Jobe adati unduna wa zaumoyo uli ndi mavuto a nkhaninkhani ofuna kuthana nawo, koma kuti izi zitheke boma likuyenera kuonjezera ndalama zomwe lapereka ku undunawu.

“Izi zithandizanso kuti boma likwaniritse ndondomeko yake ya chitukuko ya  Malawi Growth and Development Strategy [MGD] III,” iye adatero.

MGD III ndi mndandanda wa mfundo ndi ndondomeko zotukulira dziko lino.

“M’zipatala zathu muli mavuto akusowa kwa mankhwala, zipangizo zogwirira ntchito, komanso anthu ogwira ntchito ndi operewera. Zonsezi zikulira ndalama,” adatero Jobe.

Gumba adati komiti yake igwira ntchito ndi unduna wa zachuma pofuna kuonetsetsa kuti ndalama zomwe unduna wa zaumoyo umalandira zikugwiradi ntchito yake.

“Iyi ndi ntchito yathu chifukwa ndi munthu wathanzi yekha amene angatukule dziko lino,” iye adatero. n

Related Articles

Back to top button