Nkhani

Malawi siidalakwe za al-Bashir

Listen to this article

Mphunzitsi wa za mbiri yakale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Pulofesa Chijere Chirwa wati dziko lino silingakhudzidwe m’njira iliyonse pokana kuchititsa msonkhono wa mgwirizano wa maiko a mu Africa.

Mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adaletsa kuti msonkhanowu usachitikenso m’dziko muno chifukwa chokakamizidwa kuti limange mtsogoleri wa dziko la Sudan, Omar Hassan al-Bashir.

Mkuluyu wakhala akusakidwa ndi bwalo loona milandu ya upandu padziko lapansi la International Criminal Court (ICC) pamilandu ya upandu.

Dziko lino limayembekezereka kuchititsa msonkhanowo kuyambira pa 9 mpaka pa 16 mwezi wa mawa ku Lilongwe.

Sabata ziwiri zapitazo, Banda adanenetsa kuti ngati al-Bashir angayerekeze zobwera m’dziko muno adzamangidwa.

Koma akuluakulu a mgwirizanowo adati Malawi monga dziko lomwe lichititse msonkhanowo likuyenera kulandira munthu aliyense yemwe ndi membala wa mgwirizanowo.

Izi zidasokoneza Banda popeza omwe amathandiza dziko lino adanenetsa kuti dziko lino limange al-Bashir akatera m’dziko muno.

Banda adalengeza kuti sachititsanso msonkhanowo ndipo m’malo mwake msonkhanowo uchitikira m’dziko la Ethiopia.

Koma Chirwa wati ganizo la Banda lili bwino ndipo silingaike dziko lino pamoto.

“Ubwino wake n’kuti pali maiko ena monga Zambia ndi Botswana omwe ali mumgwirizanowo koma adaneneratu kuti amanga mkuluyu akafika m’dziko lawo.

“Ichi ndichitsimikizo kuti sitidalakwitse chifukwa maiko ena amagwirizana ndi ganizo lathu lomanga mkuluyo,” adatero Chirwa.

Related Articles

Back to top button